Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Nsagwada za Ng’ona

Nsagwada za Ng’ona

PA DZIKO LAPANSI palibe nyama yoluma mwamphamvu ngati ng’ona. Mwachitsanzo, ng’ona ina ya ku Australia ikaluma, mphamvu zake tingaziyerekezere ndi mphamvu za kuluma kwa mkango ndiyeno n’kuziwirikiza katatu. Koma nsagwadazi zikakhudzidwa, ng’onayo imazindikira mwamsanga kuposa mmene ifeyo timamvera tikakhudzidwa chala. Popeza khungu la ng’ona limakhala ngati chikhungwa, kodi zimenezi zimatheka bwanji?

Nsagwada zake zimakhala ndi timinyewa tina ting’onoting’ono timene timaithandiza. Katswiri wina dzina lake Duncan Leitch anachita kafukufuku wa timinyewa timeneti. Anati, “Timinyewati timachokera penapake m’chibade cha mutu wake.” Timasanjidwa m’njira yoti tikhale totetezeka komanso kuti ng’onayo izizindikira mwamsanga zinthu zimene zili m’kamwa. Choncho sivutika kudziwa kuti ichi n’chakudya, izi n’zinyalala. Ng’ona imathanso kutenga ana ake m’kamwa mwake osawaluma. Choncho tingati nsagwada za ng’ona n’zodabwitsa kwambiri.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti ng’ona ikhale ndi nsagwada zotere, kapena pali winawake amene anailenga?