Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Georgette Douwma/Stone via Getty Images

KODI DZIKOLI LIDZAKHALANSO BWINO?

Nyanja Zikuluzikulu

Nyanja Zikuluzikulu

M’NYANJA zikuluzikulu ndi mmene mumachokera chakudya chochuluka chimene timadya komanso zinthu zambiri zimene zimafunika popanga mankhwala. M’nyanjazi ndi mmenenso mumachokera mpweya wa okosijeni wopitirira hafu ya mpweya wonse womwe umagwiritsidwa ntchito padziko lonse. Komanso kuwonjezera pamenepo, nyanjazi zimathandiza kuti nyengo iziyenda bwino padzikoli.

Chifukwa Chake Tikufunika Kuteteza Nyanjazi

Kusintha kwa nyengo kwachititsa kuti zinthu zam’madzi zotchedwa coral reefs, komanso zamoyo zina zam’madzi zikhale pa chiopsezo. Asayansi amanena kuti pafupifupi ma coral reefs onse, omwe amathandiza zamoyo pafupifupi 25 pa 100 zilizonse zodziwika zam’madzi, ali pachiopsezo choti akhoza kufa m’zaka 30 zikubwerazi.

Akatswiri amanena kuti pafupifupi 90 peresenti ya mbalame zakunyanja zimadya mapulasitiki ndipo zikuoneka kuti mapulasitiki amene amapezeka m’nyanja amapha zamoyo mamiliyoni ambiri chaka chilichonse.

Mu 2022, mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations a António Guterres ananena kuti, “Anthufe tasiya kusamalira nyanja ndipo panopa tinganene kuti nyanja zili pachiopsezo.”

Dzikoli Linapangidwa M’njira Yoti Lizitha Kudzikonza Lokha

Nyanja komanso zamoyo zimene zimakhalamo zinakonzedwa m’njira yoti zizitha kudzikonza zokha kuti m’nyanjamo muzikhala mwaukhondo komanso zamoyozo zizikhala zathanzi ngati sizikusokonezedwa ndi zochita za anthu. Buku lina linanena kuti, “ngati mbali inayake ya nyanja ili yotetezedwa kuti anthu asaiwononge, nyanjayo imakwanitsa kudziyeretsa yokha.” (Regeneration: Ending the Climate Crisis in One Generation.) Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  • Tizomera tina ting’onoting’ono tam’madzi, timachotsa ndi kusunga mpweya wa kaboni dayokisaidi umene umachititsa kuti padzikoli pazitentha kwambiri. Tizomerati timasunga mpweyawu wochuluka mofanana ndi mpweya wonse wa kaboni dayokisaidi womwe umasungidwa ndi mitengo, maudzu komanso zomera zina zonse zapamtunda.

  • Tizilombo tina ting’onoting’ono ta m’nyanja timadya nsomba zimene zafa, zomwe zikanapangitsa kuti nyanja iwonongeke. Kenako tizilombo ting’onoting’onoti timadyedwa ndi zamoyo zina zam’madzi. Webusaiti ina imanena kuti, “zimenezi zimachititsa kuti m’nyanja muzikhala moyera komanso mooneka bwino.”—Smithsonian Institution Ocean Portal.

  • Zamoyo zambiri zam’madzi zimagaya bwino chakudya, zomwe zimathandiza kuti m’madzimo musamakhale asidi wambiri yemwe amawononga ma coral reefs, nsomba ndi zamoyo zina.

Zimene Anthu Akuchita Kuti Athetse Vutoli

Kugwiritsa ntchito zikwama komanso mabotolo amene tingawagwiritse ntchito kwa nthawi yaitali kungathandize kuchepetsa zinyalala za pulasitiki zomwe zimapezeka m’nyanja.

M’nyanja simungafunike kukonzedwa ngati simunalowe zinyalala. Akatswiri amalimbikitsa kuti anthu azigwiritsa ntchito zinthu monga zikwama, zipangizo zina komanso makontena mobwerezabwereza m’malo mogwiritsa ntchito zinthu zapulasitiki kamodzi n’kuzitaya.

Koma zimenezi si zokwanira. Posachedwapa, m’chaka chimodzi chokha, bungwe lina loona zachilengedwe linatolera zinyalala zochuluka matani pafupifupi 8,300 zomwe zinatayidwa m’mphepete mwa nyanja m’mayiko 112. Komatu limeneli linali gawo limodzi mwa magawo 1,000 a zinyalala amene amatayidwa m’nyanja chaka chilichonse.

A National Geographic ananena kuti, “anthu awononga kwambiri nyanja moti zimene achita pofika pano sizingakonzedwe. Anthu akugwiritsa ntchito kwambiri zinthu monga gasi, oilo komanso malasha moti nyama zam’madzi zikulephera kugwira ntchito yake yoyeretsa nyanja monga mmene zinakonzedwera. Anthufe tikulakwitsa kwambiri.”

Kodi Baibulo Limatipatsa Chiyembekezo Chotani?

“Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga. Pali nyanja, yomwe ndi yakuya komanso yaikulu kwambiri, mmene muli zamoyo zosawerengeka, zazikulu ndi zazing’ono zomwe.”—Salimo 104:​24, 25.

Mlengi wathu anapanga nyanja m’njira yakuti zizidziyeretsa zokha. Taganizirani izi: Ngati amadziwa zinthu zambiri zokhudza nyanja komanso zinthu zonse zamoyo zimene zimakhalamo, kodi sitinganene kuti ali ndi mphamvu zoti angathe kukonzanso nyanjazi? Onani nkhani yakuti “Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino,” patsamba 15.