Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA

Mfundo Zofunika Kwambiri Kwa Anthu Omwe Aferedwa

Mfundo Zofunika Kwambiri Kwa Anthu Omwe Aferedwa

OCHITA KAFUKUFUKU AKHALA AKUFUFUZA NJIRA ZOTHANDIZIRA ANTHU OMWE AKUVUTIKA NDI IMFA YA WACHIBALE KAPENA MNZAWO. Komabe, monga mmene tinafotokozera m’nkhani yapitayi, mfundo zothandiza zomwe akatswiriwa amapereka zimagwirizana ndi zomwe Baibulo limanena. Ndipotu Baibulo limapereka malangizo othandiza kwambiri. Malangizo ake amakhala olimbikitsa anthu omwe aferedwa ndipo sitingawapeze kulikonse.

  • Timadziwa kuti achibale ndi anzathu omwe anamwalira sakuvutika

    Pa Mlaliki 9:5, Baibulo limanena kuti: “akufa sadziwa chilichonse.” Limanenanso kuti: “zimene anali kuganiza zimatheratu.” (Salimo 146:4) Mogwirizana ndi mfundozi, Baibulo limayerekezera munthu amene wamwalira ndi amene ali m’tulo.​—Yohane 11:11.

  • Timatonthozedwa kwambiri tikamakhulupirira Mulungu

    Pa Salimo 34:15, Baibulo limati: “Maso a Yehova * ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” Tikamapemphera kwa Mulungu ndi kumuuza mmene tikumvera mumtima, timamva bwino ndipo maganizo athu amayamba kukhala m’malo. Kupemphera kumatithandizanso kuti tikhale paubwenzi ndi Mlengi wathu amene amagwiritsa ntchito mphamvu zake potitonthoza.

  • Zinthu zabwino zomwe tikuyembekezera m’tsogolo

    Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kudzaonanso anthu onse omwe anamwalira atakhalanso ndi moyo. Mavesi angapo m’Baibulo amafotokoza mmene zinthu zidzakhalire nthawi imeneyo. Mwachitsanzo, Baibulo limafotokoza kuti Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Anthu ambiri omwe amakhulupirira Yehova, amatonthozedwa chifukwa chokhala ndi chiyembekezo chakuti adzaonananso ndi okondedwa awo omwe anamwalira. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Ann amene mwamuna wake wazaka 65 anamwalira, ananena kuti: “Ndimalimbikitsidwa chifukwa Baibulo limanena kuti anthu omwe anamwalira sakuvutika komanso kuti Mulungu adzaukitsa anthu onse omwe akuwakumbukira. Mfundo zimenezi zimandilimbikitsa ndikayamba kuganiza za mwamuna wanga ndipo zimandithandiza kuti ndipirire.”

Tiina amene tamutchula m’nkhani yoyambirira, ananena kuti: “Kungochokera pomwe mwamuna wanga Timo anamwalira, Mulungu wakhala akundithandiza. Ndikasokonezeka kwambiri maganizo ndimaona kuti Yehova ali nane. Ndimayembekezera mwachidwi kudzaona akufa akuukitsidwa. Zimenezi zimandilimbikitsa kuti ndisafooke mpaka pomwe ndidzaonanenso ndi mwamuna wangayu.”

Kuwonjezera pa Ann ndi Tiina, palinso anthu ambiri omwe amakhulupirira kuti zomwe Baibulo limanenazi zidzachitikadi. Ngati mukuona kuti zimene Baibulo limanena ndi nthano kapena nkhambakamwa chabe, mutha kufufuza kuti mupeze umboni wotsimikizira kuti zomwe limanena zidzachitikadi. Mwina mwaona kale kuti lili ndi mfundo zothandiza anthu omwe aferedwa.

DZIWANI ZAMBIRI ZOMWE ZIDZACHITIKIRE ANTHU OMWE ANAMWALIRA

Onerani mavidiyo ogwirizana ndi nkhaniyi pa webusaiti ya jw.org

Baibulo limanena kuti m’tsogolomu tidzakumananso ndi okondedwa athu omwe anamwalira

KODI CHIMACHITIKA N’CHIYANI MUNTHU AKAMWALIRA?

Kodi chimachitika n’chiyani anthufe tikafa? Zomwe Baibulo limanena pa nkhaniyi zimatitonthoza

Onani pomwe alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Tsegulani Mbali Yakuti: Baibulo

KODI MUNGAKONDE KUMVA UTHENGA WABWINO?

Masiku ano nkhani zoipa zili ponseponse. Koma kodi uthenga wabwino tingaupeze kuti? Vidiyoyi ikufotokoza za kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu.

Onani pomwe alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Tsegulani Mbali Yakuti: Misonkhano ndi Utumiki Wathu

^ ndime 7 Yehova ndi dzina la Mulungu lomwe limapezeka m’Baibulo.