Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifukwa Chake Yankho la Funsoli Ndi Lofunika

Chifukwa Chake Yankho la Funsoli Ndi Lofunika

N’chifukwa chiyani n’zofunika kudziwa ngati kuli Mlengi? Ngati mukukhutira ndi umboni wakuti kuli Mulungu yemwe ndi wamphamvuyonse, ndiye kuti mungakonde kuonanso umboni wakuti Baibulo linauziridwa ndi iye. Ngati mukukhulupirira zimene Baibulo limanena, zikhoza kukuthandizani m’njira zotsatirazi:

Mudzayamba kusangalala kwambiri ndi moyo wanu

BAIBULO LIMANENA KUTI: “[Mulungu] anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.”​—Machitidwe 14:17.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Zinthu zonse zimene timasangalala nazo m’chilengedwechi ndi mphatso zochokera kwa Mlengi. Mukhoza kuyamikira kwambiri mphatso zimenezi mukazindikira kuti amene anazipereka amakuganizirani.

Mudzapeza malangizo odalirika amene angakuthandizeni

BAIBULO LIMANENA KUTI: “Udzamvetsa zinthu zolondola, zolungama, zowongoka, ndiponso njira yonse ya zinthu zabwino.”​—Miyambo 2:9.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Monga Mlengi wanu, Mulungu amadziwa zimene mumafunikira kuti muzisangalala. Mukamawerenga Baibulo, mukhoza kuphunzira zinthu zimene zingakuthandizeni pa moyo wanu.

Mudzapeza mayankho a mafunso anu

BAIBULO LIMANENA KUTI: “Udzamudziwadi Mulungu.”​—Miyambo 2:5.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Kudziwa kuti Mlengi alipo kungakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri monga: Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiyani timavutika? Kodi chimachitika n’chiyani tikamwalira? Mukhoza kupeza mayankho ogwira mtima m’Baibulo.

Mudzakhala ndi chiyembekezo cha zinthu za m’tsogolo

BAIBULO LIMANENA KUTI: “‘Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino,’ watero Yehova.”​—Yeremiya 29:11.

KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?: Mulungu akulonjeza kuti m’tsogolomu adzachotsa zinthu zoipa, adzathetsa mavuto komanso imfa. Mukamakhulupirira malonjezo a Mulungu, chiyembekezo chanu cha zinthu za m’tsogolo chidzakuthandizani kupirira molimba mtima mavuto amene mumakumana nawo tsiku ndi tsiku.