Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Kuphunzitsa Mwana Wanu Nkhani Zokhudza Kugonana

Kuphunzitsa Mwana Wanu Nkhani Zokhudza Kugonana

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Kale ana ankayambira kumva kwa makolo awo nkhani zokhudza kugonana ndipo makolowo ankawaphunzitsa nkhanizi mwapang’onopang’ono mogwirizana ndi msinkhu wawo.

Koma masiku ano zinthu zinasintha. Izi zili choncho chifukwa cha zimene buku lina limanena. Limati: “Masiku ano ana aang’ono kwambiri amatha kuona zinthu zolaula chifukwa zinthu zokhudza kugonana zayamba kuchuluka mu zinthu zimene ana amawerenga kapena kuonera.” (The Lolita Effect) Kodi zimenezi zimathandiza anawo kapena zimawasokoneza?

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Zinthu zolaula zili paliponse. Wolemba mabuku wina, dzina lake Deborah Roffman, analemba kuti: “Zinthu zolaula komanso mawu okhudza kugonana zikupezeka m’mafilimu, mabuku, nyimbo, mapulogalamu a pa TV, mameseji, masewera, zikwangwani, zithunzi zapakompyuta kapena pafoni komanso m’zimene anthu amalankhula akamacheza kapena kutsatsa malonda. Izi zimachititsa kuti [achinyamata ndiponso ana aang’ono] aziona kuti kugonana . . . ndi kofunika kwambiri pa moyo wawo kuposa chilichonse.”—Talk to Me First.

Otsatsa malonda nawonso akusokoneza achinyamata. Anthu ogulitsa zinthu amatsatsa zovala za ana zowachititsa kuti azioneka mokopa ena. Zimenezi zimaphunzitsa ana kuti aziganizira kwambiri za maonekedwe awo. Buku lina limati: “Otsatsa malonda amakonda kukopa ana chifukwa amadziwa kuti akhoza kutengeka mosavuta. Koma sikuti amagwiritsa ntchito zinthu zokhudza kugonana n’cholinga choti anawo azilakalaka kugonana koma kuti angogulitsa zimene akutsatsazo.”—So Sexy So Soon.

Kungodziwa zinthu si kokwanira. Kungodziwa mmene galimoto imagwirira ntchito sikutanthauza kuti mungakhale woyendetsa wodalirika. N’chimodzimodzinso ndi kudziwa nkhani zokhudza kugonana. Kungodziwa nkhani zimenezi sikutanthauza kuti mungasankhe zinthu mwanzeru pa nkhaniyi.

Mfundo yofunika kwambiri: Masiku ano n’kofunika kwambiri kuti muziphunzitsa ana anu kuti azigwiritsa ntchito “mphamvu zawo za kuzindikira” n’cholinga choti azitha “kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”—Aheberi 5:14.

ZIMENE MUNGACHITE

Muzikambirana nawo. Mwina zingakhale zovuta kukambirana ndi ana anu nkhani zokhudza kugonana. Komabe muyenera kudziwa kuti ndi udindo wanu ndipo muyenera kuukwaniritsa.—Lemba lothandiza: Miyambo 22:6.

Musamawapanikize ndi zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. M’malo mokambirana kwa nthawi yaitali, muziyesetsa kulankhula nawo mocheza mukamayenda kapena kugwira ntchito inayake. Muziwafunsa mafunso othandiza kuti amasuke n’kumakuuzani zakukhosi kwawo. Mwachitsanzo, m’malo mongofunsa kuti, “Kodi iweyo umakonda zithunzi ngati zimenezo?” ndi bwino kufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani anthu amagwiritsa ntchito zithunzi ngati zimenezo potsatsa malonda?” Akayankha, mungamufunsenso kuti, “Nanga iweyo umaziona bwanji?”—Lemba lothandiza: Deuteronomo 6:6, 7.

Muzikambirana nawo mogwirizana ndi msinkhu wawo. Mungaphunzitse ana aang’ono mayina olondola a ziwalo zogonanira komanso zimene angachite podziteteza kwa anthu ogwiririra ana. Ana akamakula makolo angawaphunzitse zinthu zosavuta kumvetsa zokhudza kugonana ndiponso kubereka ana. Koma anawo asanathe msinkhu, makolo ayenera kuwathandiza kuti amvetse bwino zinthu zambiri zokhudza kugonana komanso mmene angasankhire zinthu mwanzeru pa nkhaniyi.

Muziwaphunzitsa makhalidwe abwino. Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kuyambira ali aang’ono makhalidwe abwino monga kulankhula zoona, kukhala okhulupirika komanso kulemekeza anthu ena. Kuchita zimenezi kungathandize kuti anawo akadzaphunzitsidwa za kugonana adzamvetse zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita pa nkhaniyi. Makolo ayeneranso kuuza ana awo mosapita m’mbali mfundo zimene amayendera pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, ayenera kuwauza ngati amaona kuti n’kulakwa kuti munthu agonane ndi wina asanalowe m’banja. Ayeneranso kuwafotokozera chifukwa chake amaona kuti kuchita zimenezi n’kulakwa komanso mavuto ake. Buku lina limati: “Achinyamata ambiri amene amadziwa kuti makolo awo amaona kuti n’kulakwa kugonana asanalowe m’banja amapewa kugonana.”—Beyond the Big Talk.

Muzikhala chitsanzo chabwino. Muzitsatira mfundo zimene mumaphunzitsa ana anu. Muyenera kudzifunsa kuti, Kodi ndimaseka munthu wina akanena nthabwala zokhudza kugonana? Nanga kodi ndimavala kapena kuchita zinthu zofuna kukopa ena? Ngati mumachita zimenezi, ana anu sangatsatire mfundo zabwino zimene mumawaphunzitsa.—Lemba lothandiza: Aroma 2:21.

Musamangowauza kuti kugonana n’koipa. Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo kungakhale kosangalatsa kwambiri kwa anthu amene ali pa banja. (Miyambo 5:18, 19) Muziuza mwana wanu kuti iyenso adzatha kusangalala ndi kugonana akadzalowa m’banja popanda kukumana ndi mavuto omwe angabwere akagonana ndi munthu wina panopa.—1 Timoteyo 1:18, 19.