Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULANDIRA MPHATSO YAIKULU IMENE MULUNGU WAPEREKA?

Mphatso Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse

Mphatso Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse

WACHIKULIRE wina anapatsa Jordan chosongolera mapensulo chooneka ngati boti. Mphatsoyi ikhoza kuoneka ngati yachabechabe koma Jordan amaikonda kwambiri. Iye anati: “Wachikulire wina amene ankagwirizana ndi banja lathu, dzina lake Russell, anandipatsa ndili wamng’ono kwambiri.” Wachikulireyu atamwalira, Jordan anamva kuti ankalimbikitsa kwambiri agogo ake komanso makolo ake pa nthawi yovuta. Jordan anati: “Panopa mphatsoyi ndimaiona kuti ndi yamtengo wapatali kwambiri chifukwa cha zinthu zabwino zimene ndamva zokhudza Russell.”

Nkhaniyi ikusonyeza kuti mphatso ikhoza kuoneka ngati yachabechabe kwa anthu ena. Koma munthu amene wailandira akhoza kuona kuti ndi yofunika kwambiri. Baibulo limafotokoza za mphatso yoposa zonse. Limanena kuti: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16.

Mphatsoyi ingathandize munthu amene wailandira kuti akapeze moyo wosatha. Kunena zoona, palibe mphatso ina imene ingapose mphatso imeneyi. Anthu ena sazindikira kufunika kwake koma Akhristu enieni amadziwa kuti ndi ‘yamtengo wapatali.’ (Salimo 49:8; 1 Petulo 1:18, 19) N’chifukwa chiyani Mulungu anapereka Mwana wake?

Zimene mtumwi Paulo analemba zikuyankha funsoli. Iye anati: “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse.” (Aroma 5:12) Adamu, yemwe anali munthu woyamba, sanamvere Mulungu ndipo chilango chake chinali imfa. Choncho kudzera mwa Adamu, imfa inafalikira kwa anthu onse padzikoli.

Baibulo limanenanso kuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Pofuna kupulumutsa anthu, Mulungu anatumiza Mwana wakeyo kuti apereke moyo wake wangwiro ngati nsembe. Nsembeyi imatchedwa “dipo” ndipo aliyense wokhulupirira Yesu adzapeza moyo wosatha.—Aroma 3:24.

Pofotokoza madalitso amene Mulungu akupereka kwa anthu ake kudzera mwa Yesu Khristu, Paulo anati: “Tikuyamika Mulungu chifukwa cha mphatso yake yaulere, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akorinto 9:15) Mphatso ya dipo ndi yapamwamba kwambiri moti sitingathe kuifotokoza bwinobwino. Koma n’chifukwa chiyani tikunena kuti mphatsoyi imaposa mphatso zonse zimene Mulungu watipatsa? * Nanga tingasonyeze bwanji kuti timaiyamikira? Werengani nkhani ziwiri zotsatira kuti mumve mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso amenewa.

^ ndime 8 Yesu ndi amene “anapereka moyo wake chifukwa cha ife.” (1 Yohane 3:16) Koma popeza nsembeyi inali mbali ya cholinga cha Mulungu, nkhanizi zalembedwa m’njira yosonyeza kuti Mulungu ndi amene anapereka dipo.