Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Malonjezo Amene Adzakwaniritsidwe

Malonjezo Amene Adzakwaniritsidwe

Uthenga wabwino wa Ufumu ukulalikidwa padziko lonse lapansi monga mmene Yesu ananenera. (Mateyu 24:14) Buku la Danieli limanena kuti Ufumu umenewu ndi boma la Mulungu. Chaputala 2 cha bukuli chili ndi ulosi wonena za maboma, kapena kuti maufumu, osiyanasiyana omwe akhala akulamulira padzikoli kuyambira ndi ufumu wa Babulo mpaka umene ukulamulira masiku ano. Ponena za zimene zidzachitike m’tsogolo, vesi 44 limanena kuti:

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”

Ulosi umenewu komanso maulosi ena a m’Baibulo amasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa maboma a anthu ndipo udzabweretsa mtendere padziko lonse lapansi. Kodi moyo udzakhala wotani mu Ufumuwu? Taonani ena mwa malonjezo osangalatsa kwambiri amene akwaniritsidwe posachedwapa.

  • SIPADZAKHALANSO NKHONDO

    Salimo 46:9: “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”

    Tangoganizani mmene moyo ukanakhalira zikanakhala kuti ndalama zonse zimene anthu amagwiritsa ntchito popanga zida zankhondo amazigwiritsa ntchito pothandiza anthu kuti azikhala ndi moyo wabwino. Lonjezo loti sipadzakhalanso nkhondo lidzakwaniritsidwa mu Ufumu wa Mulungu.

  • SIPADZAKHALANSO MATENDA

    Yesaya 33:24: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”

    Taganizirani mmene zidzakhalire matenda onse akadzatha! Palibe amene azidzavutika ndi matenda a mtima, khansa, malungo komanso matenda ena. Pa nthawiyo sipadzafunikanso mankhwala komanso kumanga zipatala. Baibulo limasonyeza kuti anthu amene adzakhale padzikoli adzakhala athanzi.

  • SIPADZAKHALANSO NJALA

    Salimo 72:16: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”

    Padzikoli padzakhala chakudya chokwanira munthu aliyense. Njala komanso matenda osowa zakudya m’thupi zidzakhala mbiri yakale.

  • SIPADZAKHALANSO ZOPWETEKA, CHISONI KOMANSO IMFA

    Chivumbulutso 21:4: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

    Izi zikusonyeza kuti anthu adzakhala m’paradaiso kwamuyaya. Zimenezi ndi zimene Mlengi wathu, Yehova, watilonjeza.

“ADZAKWANIRITSADI ZIMENE NDINAWATUMIZIRA”

Kodi mukuganiza kuti zimene tafotokozazi zingadzachitikedi? Anthu ambiri amaona kuti malonjezo a m’Baibulowa ndi abwino kwambiri. Koma ena amaona kuti mfundo yoti anthu adzakhale ndi moyo kwamuyaya ndi yovuta kumvetsa. Zimenezi si zodabwitsa, chifukwa palibe munthu amene anakhalapo ndi moyo wotere kuti atifotokozere mmene umakhalira.

Anthu akhala akuvutika ndi uchimo komanso imfa ndipo ambiri anafika pongozolowera mavutowo n’kumaona kuti ndi mmene moyo uyenera kukhalira. Koma zimenezi si zimene Mlengi wathu Yehova ankafuna pamene ankalenga anthu.

Pofuna kutithandiza kudziwa kuti zimene walonjezazi zidzachitikadi, Mulungu ananena motsimikiza za Mawu ake kuti: “Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma adzachitadi zimene ine ndikufuna ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:11.

Baibulo limanena kuti Yehova ndi Mulungu “amene sanganame.” (Tito 1:2) Popeza watilonjeza kuti adzatichitira zinthu zonsezi, tingachite bwino kuganizira mafunso awa: Kodi n’zotheka kuti anthu adzakhale ndi moyo kwamuyaya m’Paradaiso padzikoli? Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzalandire nawo madalitso amenewa? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi kuti mupeze mayankho a mafunso amenewa.