Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi mukhoza kuthandiza ena posatengera msinkhu wawo, dziko limene akuchokera kapena chipembedzo chawo?

Anthu Amene Amathandiza Ena Amalandira Madalitso

Anthu Amene Amathandiza Ena Amalandira Madalitso

Padziko lonse anthu ambiri amasowa chakudya ndi pokhala. Ena ali ndi zinthu zimenezi koma amasowa chiyembekezo chabwino chokhudza tsogolo lawo. Mulungu amafuna kuti tizithandiza anthu oterewa ndipo adzatidalitsa tikamachita zimenezi.

ZIMENE MALEMBA OPATULIKA AMANENA

“Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.”​—MIYAMBO 19:17.

ZIMENE KUTHANDIZA ENA KUMATANTHAUZA

Yesu anafotokoza nkhani yokhudza munthu amene achifwamba anamuvulaza n’kumusiya atatsala pang’ono kufa. (Luka 10:29-37) Munthu wina wachifundo yemwe sankadziwana ndi munthu wovulazidwayo anaima n’kumuthandiza. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti anali osiyana mitundu.

Kuwonjezera pa kutsuka mabala a munthu wovulala ndi kumupatsa zinthu zina zofunikira, munthu wachifundoyu analimbikitsa ndi kutonthoza wovulalayo ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti asakhalenso ndi nkhawa.

Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani? Yesu anatiphunzitsa kuti tiziyesetsa kuchita zimene tingakwanitse pothandiza ena. (Miyambo 14:31) Malemba Opatulika amatiuza kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa umphawi ndi kuvutika. Komabe mwina tingadzifunse kuti, Kodi Mulungu adzachita liti zimenezi nanga adzazichita bwanji? Nkhani yotsatirayi ifotokoza madalitso amene Mlengi wanu wachikondi wakulonjezani.