Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ntchito Zanu Zichulukadi, Yehova!”

“Ntchito Zanu Zichulukadi, Yehova!”

Kukongola kwa Chilengedwe cha Yehova

“Ntchito Zanu Zichulukadi, Yehova!”

KAYA timakhala kumudzi kapena mu mzinda, kumapiri kapena kufupi ndi nyanja, tazunguliridwa ndi chilengedwe chokongola ndiponso chochititsa nthumanzi. Mogwirizana ndi zimenezi, Kalendala ya 2004 ya Mboni za Yehova ili ndi zithunzi zosiyanasiyana za zinthu zochititsa chidwi zimene Yehova Mulungu analenga.

Anthu amene amayamikira zimenezi, nthawi zonse akhala akusinkhasinkha za zinthu zimene Mulungu analenga. Mwachitsanzo, taganizirani za Solomo, amene nzeru zake zinaposa “nzeru za anthu onse a kum’mawa.” Baibulo limati iye ankakamba “za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebano kufikira hisopi wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.” (1 Mafumu 4:30, 33) Bambo ake a Solomo, Mfumu Davide, nthawi zambiri ankasinkhasinkha za zinthu zochititsa chidwi kwambiri zimene Mulungu anapanga. Zimenezi zinam’khudza mtima moti anauza Mlengi wake kuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”​—Salmo 104:24. *

Nafenso tingachite bwino titamayang’anitsitsa chilengedwe n’kumachiganizira. Mwachitsanzo, ‘tingakweze maso athu kumwamba,’ n’kufunsa kuti: ‘Ndani analenga zimenezi?’ Amene anazilenga ndi Yehova Mulungu, amene “mphamvu zake [zili] zazikulu” ndipo alidi “wolimba mphamvu.”​—Yesaya 40:26.

Kodi kusinkhasinkha za chilengedwe cha Yehova kuyenera kutikhudza motani? Mwa zina, kuyenera kutikhudza m’njira zitatu. Kuyenera (1) kutikumbutsa kuti tizisamalira ndi kukonda kwambiri moyo wathu, (2) kutilimbikitsa kuthandiza ena kuti aphunzire ku chilengedwe, ndiponso (3) kutilimbikitsa kuphunzira zambiri za Mlengi wathu ndi kumudziwa bwino.

Popeza moyo wa ife anthu ndi wapamwamba kwambiri kuposa wa nyama “zopanda nzeru,” timatha kuyang’anitsitsa chilengedwe chodabwitsa ndi kuchiyamikira. (2 Petro 2:12) Maso athu amatha kuona malo okongola. Makutu athu amatha kumva nyimbo za nthetemya za mbalame. Ndipo luso lotha kudziwa nthawi ndi kumalo kumene tili limatithandiza kukumbukira zinthu zosangalatsa zimene zinachitika m’mbuyomu. Ngakhale kuti moyo wamasiku ano uli ndi mavuto ake, umasangalatsabe!

Makolo amasangalala kuona kuti ana awo mwachibadwa amakopeka ndi chilengedwe. Ana amakonda kwambiri kusewera ndi tianapiye ta nkhuku, tiana ta galu, kapena kukwera mu mtengo. Makolo angachite bwino kuthandiza ana awo kuona kugwirizana kwa chilengedwe ndi Mlengi. Ana akayamba kulemekeza chilengedwe cha Yehova ndi kuchita nacho nthumanzi akadali aang’ono, akhoza kupitirizabe kuchiona motero mpaka moyo wawo wonse.​—Salmo 111:2, 10.

Tingakhale anthu osaona zinthu bwinobwino titati tizichita kaso ndi chilengedwe koma n’kulephera kuyamikira Mlengi. Ulosi wa Yesaya umatithandiza kuganizira mfundo imeneyi pamene umati: “Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.”​—Yesaya 40:28.

Zoonadi, ntchito za Yehova zimatipatsa umboni wa nzeru zake zosasanthulika, mphamvu zake zosafanana ndi za wina aliyense, ndi chikondi chake chachikulu pa ife. Tikaona kukongola kwa chilengedwe ndi kumvetsa makhalidwe a Amene analenga zonsezo, tiyeni tizigwirizana ndi mawu amene Davide ananena, oti: “Palibe wina wonga Inu, Ambuye; ndipo palibe ntchito zonga zanu.”​—Salmo 86:8.

Tili ndi chikhulupiriro kuti anthu omvera adzapitiriza kukopeka ndi chilengedwe cha Yehova. Tidzakhala ndi nthawi yopanda malire yophunzira zambiri za Yehova mpaka muyaya. (Mlaliki 3:11) Ndipo tikadzaphunzira zambiri za iye, m’pamenenso tidzamukonde kwambiri Mlengi wathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Kalendala ya 2004 ya Mboni za Yehova, November/​December.

[Bokosi patsamba 9]

Kulemekeza Mlengi

Asayansi ambiri amene amayamikira chilengedwe amazindikira kuti Mulungu ndi amene anachilenga. Pansipa pali zitsanzo zingapo:

“Sayansi yanga imakhala yatanthauzo ndi yosangalatsa panthawi za apo ndi apo pamene ndimatulukira chinthu chatsopano ndipo ndimanena kuti, ‘Kodi umu ndi mmene Mulungu anapangira zimenezi eti?’ Cholinga changa n’choti ndimvetseko mbali yaing’ono ya mapulani a Mulungu.”​—Anatero Henry Schaefer, pulofesa wa sayansi ya mmene zinthu zinapangidwira.

“Ponena za mmene thambo linakhalirako, makamaka chimene chimapangitsa kuti lizifutukuka, wowerenga aliyense ayenera kudzipezera yekha yankho lake, koma sitingamvetse bwino zimenezi popanda Iyeyo [Mulungu].”​—Anatero Edward Milne, katswiri wopenda chilengedwe wa ku Britain.

“Tikudziwa kuti chilengedwe chimatha kufotokozedwa ndi masamu apamwamba kwambiri chifukwa choti Mulungu anachilenga.”​—Anatero Alexander Polyakov, katswiri wa masamu wa ku Russia.

“Tikamafufuza zinthu zachilengedwe, timakhala tikuphunzira maganizo a Mlengi, kuzindikira zimene anapanga, kumasulira zinthu Zake, osati zathu.”​—Anatero Louis Agassiz, katswiri wa sayansi ya zinthu zamoyo wa ku America.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mbalame za ku Antarctic Peninsula

[Chithunzi patsamba 9]

Grand Teton National Park, ku Wyoming, ku United States

[Mawu a Chithunzi]

Jack Hoehn/​Index Stock Photography