Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tili M’nthawi Yovuta

Tili M’nthawi Yovuta

Tili M’nthawi Yovuta

BAIBULO linalosera kuti anthu adzakhala mu “nthawi yovuta yoikika.” Limati nthawi imeneyi ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5; 2 Petulo 3:3-7) Yesu Khristu anatchulanso za nthawi yomweyi, poyankha funso limene ophunzira ake anafunsa lokhudza “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 24:3) Kodi panopo tili m’masiku otsiriza? Yankhani nokha funsoli poona zimene Baibulo linalosera n’kuziyerekezera ndi malipoti a zimene zikuchitika panopo, omwe tawalemba pamunsipa.

Zimene Baibulo linalosera: nkhondo​Luka 21:10; Chivumbulutso 6:4.

Zimene malipoti aposachedwapa anena: “Anthu amene aphedwa pa nkhondo m’zaka 100 zapitazi ndi ochuluka kuwirikiza katatu poyerekeza ndi amene anaphedwa pa zaka 1900 kuyambira pamene Yesu anali padzikoli.”​—Worldwatch Institute.

Zimene Baibulo linalosera: njala ndiponso matenda​Luka 21:11; Chivumbulutso 6:5-8.

Zimene malipoti a posachedwapa anena: “M’chaka cha 2004, akuti anthu pafupifupi 863 miliyoni padziko lonse analibe chakudya chokwanira, kusonyeza kuti anthu 7 miliyoni anawonjezeka pa chiwerengero cha chaka cha 2003.​—United Nations Food and Agriculture Organization.

Anthu okwana 1 biliyoni akukhala a m’nyumba zosalongosoka m’madera osauka kwambiri; anthu oposa 2 biliyoni ndi theka sakhala m’malo aukhondo; ndipo anthu oposa 1 biliyoni alibe madzi akumwa abwino.​—Worldwatch Institute.

Matenda a malungo akuvutitsa anthu 500 miliyoni; anthu 40 miliyoni ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a EDZI; chifuwa chachikulu cha TB chinapha anthu oposa 1 miliyoni ndi theka m’chaka cha 2005.​—World Health Organization.

Zimene Baibulo linalosera: kuwononga dziko​Chivumbulutso 11:18.

Zimene malipoti a posachedwapa anena: “Zamoyo zambiri padzikoli zawonongeka kwambiri chifukwa cha zochita za anthu, moti zina zatsala pang’ono kutheratu.” “Padziko lonse zinthu zambiri zachilengedwe zimene anthu amapindula nazo zayamba kuchepa kwambiri.”​—Millennium Ecosystem Assessment.

“Zochita za anthu zawononga kwambiri mumlengalenga moti nyengo yaipa kwambiri. Zimenezi zingathe kuwonongeratu dzikoli.”​—NASA, Goddard Institute for Space Studies.

Zimene Baibulo linanena: uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa padziko lonse​Mateyo 24:14; Chivumbulutso 14:6, 7.

Zimene malipoti a posachedwa anena: M’chaka cha 2007, Mboni za Yehova zokwana 6,957,854 zinathera maola pafupifupi 1 biliyoni ndi theka zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, m’mayiko 236.​—2008 Yearbook of Jehovah’s Witnesses.

Monga tanenera kale, Baibulo linalosera kuti m’kati mwa nthawi yovutayi padzakhala zifukwa zokwanira zokhalira ndi chiyembekezo. Yesu ananena za “uthenga wabwino” wa Ufumu wa Mulungu. Koma kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi umagwirizana bwanji ndi chiyembekezo cha anthu chodzakhala ndi tsogolo labwino? Nanga kodi Ufumu wa Mulungu udzakukhudzani motani?

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Baibulo linalosera zimene zikuchitika padzikozi