Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Yabodza Imayambitsa Bodza Linanso

Mfundo Yabodza Imayambitsa Bodza Linanso

MTUMWI Paulo anachenjeza Akhristu amene anakhala ndi moyo chakumapeto kwa nthawi ya Atumwi kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.”​—Akolose 2:8.

Ngakhale kuti Paulo anawachenjeza zimenezi, chapakati pa zaka za m’ma 100 C.E., Akhristu ena pofuna kufotokoza zikhulupiriro zawo, anayamba kutengera ziphunzitso za anthu a nzeru zapamwamba. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Iwo ankafuna kuti azikondedwa ndi anthu ophunzira a mu ufumu wa Roma komanso ankafuna kuti akope anthu ambiri.

Mmodzi wa Akhristu amenewa ndi Justin Martyr. Iye ankakhulupirira kuti munthu Wolankhula m’malo mwa Mulungu anaonekera kalekale, kwa anthu achigiriki a nzeru zapamwamba, Yesu asanabwere. Malinga ndi zimene Justin ndiponso anthu ena ankaphunzitsa, mfundo za anthu ndiponso ziphunzitso zabodza zimene zinalowa m’Chikhristu zinachititsa kuti zikhulupiriro zimenezi zifalikire padziko lonse.

Chiphunzitso chimene Justin Martyr anayambitsa chinakopa anthu ambiri. Komabe, chiphunzitso chimodzi chabodza chinapangitsa kuti pakhalenso ziphunzitso zina zabodza. Ndipo zotsatira zake n’zakuti Akhristu ambiri amakhulupirira kuti ziphunzitso zimenezi n’zoona. Kuti mutsimikizire kuti ziphunzitso zimenezi n’zabodza, yerekezerani zimene mabuku ena amanena ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.