Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tikuphunzira pa Chifundo cha Mulungu

Zimene Tikuphunzira pa Chifundo cha Mulungu

Zoti Achinyamata Achite

Zimene Tikuphunzira pa Chifundo cha Mulungu

YONA​—GAWO 2

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO​—WERENGANI YONA 3:1–4:11.

Kodi mukuganiza kuti Yona ankamva bwanji mumtima mwake pamene amalowa mumzinda wa Nineve?

․․․․․

Malinga ndi zimene Yona ananena polengeza chiweruzo cha Yehova, kodi mukuganiza kuti ankamva bwanji mumtima mwake?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Yona anavutika bwanji panthawi imene anakhala pansi kunja kwa mzinda? (Onani Yona 4:5-8.)

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yona anafuna kuti Yehova awononge mzinda wa Nineve, pokwaniritsa chenjezo limene anapereka?

․․․․․

Pogwiritsa ntchito mabuku omwe mungafufuzemo zinthu, fufuzani za (1) maonekedwe a mtengo wa msatsi ndi (2) tanthauzo la zimene mfumu ya ku Nineve inachita pofunda chiguduli ndiponso kukhala paphulusa.

․․․․․

Ngakhale kuti poyamba sanafune kukachita zimene Mulungu anam’tuma ku Nineve, n’chifukwa chiyani tinganenebe kuti Yona anali mneneri wokhulupirika komanso wolimba mtima? (Mateyo 21:28-31)

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA  . . .

Mfundo yakuti anthu angathe kusintha n’kusiya kuchita zoipa.

․․․․․

Chifundo cha Yehova.

․․․․․

Kufunika kokhala achifundo.

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Kuti mudziwe zambiri, werengani Nsanja ya Olonda ya April 1, 2009, tsamba 14 mpaka 18.

NGATI MULIBE BAIBULO, MUNGAWERENGE LA PA INTANETI PA WEBUSAITI YATHU YA www.ps8318.com.