Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amishonale Atumizidwa ‘Kukapanga Ophunzira’

Amishonale Atumizidwa ‘Kukapanga Ophunzira’

Mwambo Womaliza Maphunziro a Gileadi​—Gulu la Nambala 128

Amishonale Atumizidwa ‘Kukapanga Ophunzira’

“KUTI anthu a mitundu yonse amve uthenga wabwino, Akhristu ena anafunikira kulolera kusamuka kwawo komanso kusiya achibale awo kuti akalalikire uthenga wabwino m’dziko lina.” Amenewa ndi mawu amene m’bale David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anatsegulira nawo mwambo wosangalatsa umenewu.

Pa March 13, 2010, anthu pafupifupi 8,000 anasonkhana kuti aonerere mwambo womaliza maphunziro wa gulu la nambala 128 la Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Pamwambowu panafika alendo ochokera m’mayiko 27 ndipo ena mwa alendowa anali achibale ndi mabwenzi a anthu amene anali kumaliza maphunzirowa.

“Ophunzirawo Sanangokhala Panyumba”

M’bale Splane, yemwe anali tcheyamani wa mwambowu, anayamba ndi kufotokoza lamulo la Yesu lakuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyo 28:19, 20) Iye anagogomezera mfundo yonena kuti Yesu anatumiza ophunzira ake kwa anthu. Ndi zoona kuti pa Pentekoste mu 33 C.E., anthu ochokera ku Mesopotamiya, kumpoto kwa Africa ndi m’madera ena ambiri a mu Ufumu wa Roma anabwera ku Yerusalemu, kumene anamva uthenga wabwino. Koma wokamba nkhaniyo anafotokoza kuti ngakhale zinali choncho, “ophunzirawo sanangokhala panyumba n’kumadikira kuti anthu amitundu yonsewo achite kubwera okha. M’malomwake, anapita kumalekezero a dziko lapansi kuti akafunefune anthu.”​—Machitidwe 1:8.

M’bale Splane ananenanso kuti: “Yesu sanangowauza ophunzira ake zochita koma anawaphunzitsanso mmene angachitire zinthuzo. Sanangowauza kuti azipemphera koma anawaphunzitsa mmene ayenera kupempherera. Sanangowauza kuti azilalikira koma anawasonyeza mmene angalalikilire. Sanangowauza kuti aziphunzitsa bwino koma anawasonyeza mmene angaphunzitsire bwino anthu komanso mowafika pamtima.”

Kenako M’bale Splane analankhula kwa makolo a ophunzirawo. Iye anagwira mawu a Yesu olimbikitsa ophunzira ake akuti: “Dziwani ichi! Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 28:20) M’baleyu anatsimikizira omvera kuti Yesu adzapitiriza kusamalira ophunzirawo kulikonse kumene atumizidwa.

“Mukadzitame”

M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira anauza omaliza maphunzirowo kuti, “muzidzitama.” Iye anati pali kudzitama koyenera ndi kosayenera. Munthu wodzitama mosayenera amadzitama kuti anthu ena azimupatsa ulemu. Koma kudzitama koyenera kwafotokozedwa pa 1 Akorinto 1:31 kuti: “Amene akudzitama, adzitame mwa Yehova.” M’bale Morris ananena kuti: “Tikafuna kudzitama tizidzitama chifukwa chozindikira ndi kudziwa zozama zokhudza Yehova Mulungu. Ndipotu mwayi waukulu kwambiri umene inu ndi ine tili nawo ndi kudziwika ndi dzina loyera la Mulungu, kudziwika kuti ndife Mboni za Yehova.”​—Yeremiya 9:24.

Kenako wokamba nkhaniyo anafotokoza zimene zinachitikira mmishonale wina ku Africa, pofuna kugogomezera kufunika kouza ena za dzina la Yehova. Mmishonaleyo ndi mkazi wake anali pa ulendo wokakamba nkhani ya Baibulo. Atafika parodibuloko, msilikali wina wachinyamata anafuna kudziwa kuti m’baleyo ndi ndani ndipo anamulozetsa mfuti. Mkazi wake anakumbukira zimene anaphunzira ku sukulu ya Gilead ndipo ananong’oneza mwamuna wakeyo kuti, “Muuzeni kuti ndinu wa Mboni za Yehova ndipo mukupita kukakamba nkhani ya Baibulo.” Iye anamvera zimene mkazi wakeyo anamuuza ndipo analoledwa kupitiriza ulendo wawo. Tsiku lotsatira, m’bale ndi mlongoyo anamva pa wailesi kuti pulezidenti wa dzikolo walamula asilikali ake kuti afunefune anthu ena achiwembu amene ankadzitchula kuti ndi amishonale. Podzidziwikitsa kuti ndi Mboni za Yehova m’malo monena kuti ndi amishonale, m’bale ndi mlongoyu anapewa mavuto aakulu. M’bale Morris anamaliza nkhani yake ndi kunena kuti: “Mukapita kumene mwatumizidwa, mukadzitame. Muzidzitama chifukwa cha zonse zimene Yehova adzakwaniritsa pogwiritsa ntchito inuyo kuti aonetse ulemerero wake wosatha.”

“Kodi Mudzakwaniritsa Utumiki Wanu?”

M’bale Geoffrey Jackson amenenso ali m’Bungwe Lolamulira komanso kale anali mmishonale, analimbikitsa ophunzirawo kuganizira funso limene lili pamwambali. Iye anafunsa kuti, “Kodi tikamanena kuti munthu ndi mmishonale timatanthauza chiyani?” Kenako anafotokoza kuti mawu akuti “mmishonale” anachokera ku mawu achilatini otanthauza munthu kapena gulu la anthu limene lapatsidwa ntchito yapadera. Monga Mboni za Yehova, ntchito yathu yapadera ndiyo kulalikira uthenga wabwino ndi kuthandiza anthu mwauzimu. Timagwira ntchito imeneyi potsanzira Yesu Khristu amene nthawi zonse anali kuganizira za ntchito yake yapaderayi. Poyankha Pontiyo Pilato, amene anali bwanamkubwa wachiroma, Yesu anati: “Chimene ndinabadwira, ndi chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.”​—Yohane 18:37.

Wokamba nkhaniyo anakumbutsanso ophunzirawo za nkhani ya m’Baibulo yonena za nkhondo ya kumzinda wa Yeriko. Kwa masiku 6, Aisiraeli ankadzuka m’mamawa, kuvala zida zawo, kuzungulira Yeriko, koma kenako n’kungobwerera kunyumba. Iye anati: “Kwa anthu, zimene asilikaliwo ankachita ziyenera kuti zinkaoneka zachilendo komanso zopanda nzeru.” Anafotokozanso kuti n’kutheka kuti asilikali ena anaganiza kuti, ‘Komatu ndiye tikungotaya nthawi.’ Komabe pa tsiku la 7, Aisiraeli anauzidwa kuti azungulire mzinda wa Yeriko nthawi 7, kenako afuule mfuu yankhondo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mpanda wa mzindawo unagweratu wonse.​—Yoswa 6:13-15, 20.

M’bale Jackson anafotokoza kuti nkhaniyi ikutiphunzitsa zinthu zinayi: (1) Kumvera ndi kofunika. Tizichita zinthu motsatira njira za Yehova m’malo motsatira njira zimene ifeyo tikuona kuti ndi zabwino. (2) Tizikhulupirira Yehova. ‘Mwa chikhulupiriro, mpanda wa Yeriko unagwa,’ osati ndi zida za nkhondo. (Aheberi 11:30) (3) Tikhale odekha. Panthawi yake, madalitso a Yehova ‘adzatipeza.’ (Deuteronomo 28:2) (4) Tisatope. Musaiwale ntchito yapadera imene mwapatsidwa. M’bale Jackson anamaliza nkhani yake ndi mawu akuti, “Ngati mugwiritsa ntchito mfundo zimene takambiranazi, mudzakwaniritsadi ntchito yanu yapaderayi ndipo zimenezi zidzachititsa kuti Yehova atamandike ndi kupatsidwa ulemerero.”

Nkhani Zina Zapamwambowu

“Muzikonda Baibulo ndi Amene Analilemba.” Umenewu unali mutu wa nkhani imene Maxwell Lloyd, amene ali m’Komiti ya Nthambi ya ku United States, anakamba. Iye anauza omaliza maphunzirowo kuti: “Muzidalira kwambiri Baibulo.” Kenako anawauza mfundo zotsatirazi: Musalole kuti chikondi chanu pa Yehova Mulungu chithe. Musaganize kuti aliyense azikamvetsa zimene mukuphunzitsa. Yesetsani kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo mosavuta kuti muwafike pamtima ophunzira anu. Khalani odzichepetsa. Musamadzionetsere kuti mumadziwa zambiri. Muzikhala zitsanzo zabwino. Mukayesetse kuti ophunzira anu aziona kuti mumakonda kwambiri Baibulo.

“Onetsetsani Makwangwala.” Michael Burnett, amene ndi mmodzi wa alangizi a sukuluyi komanso amene kale anali mmishonale, anakamba nkhani ya mutu umene uli pamwambawu. Iye anafotokoza kuti nthawi zina tingamade nkhawa. Koma tizikumbukira zimene Yesu ananena kuti: “Onetsetsani makwangwala, iwo safesa mbewu kapena kukolola, . . . komatu Mulungu amawadyetsa.” (Luka 12:24) Malinga ndi Chilamulo, makwangwala anali odetsedwa, osayenera kudyedwa ndipo anayenera kuonedwa kuti ndi onyansa. (Levitiko 11:13, 15) Ngakhale kuti panthawiyo anali odetsedwa, Mulungu ankawadyetsabe. M’bale Burnett anapitiriza kuti: “Choncho mukadzakumana ndi vuto linalake m’tsogolomu, dzakumbukireni khwangwala. Ngati Mulungu ankasamalira mbalame imene inali yodetsedwa ndiponso yonyansa, kuli bwanji inuyo amene Mulungu amakuonani kuti ndinu oyera?”

“Sindikukulakwira.” Mark Noumair, amene ndi mlangizi winanso wa sukulu ya Gilead, anathandiza onse amene anali pamwambowu kuganizira mofatsa fanizo la Yesu lokhudza ogwira ntchito m’munda wa mpesa. Antchito ena anagwira ntchito tsiku lonse, pomwe ena anagwira ntchito kwa ola limodzi lokha. Koma onsewa analandira malipiro ofanana. Anthu amene anagwira ntchito nthawi yaitali aja anayamba kunyinyirika. Poyankha mmodzi wa odandaulawo, mwini mundayo anati: “Sindikukulakwira ayi. Tinapangana malipiro a dinari imodzi, si choncho kodi? Ingolandira yako uzipita.” (Mateyo 20:13, 14) Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Tisamadziyerekezere ndi anthu ena. M’bale Noumair ananena kuti: “Kudziyerekeza ndi ena mosayenerera kudzakuchititsani kukhala wosasangalala. Kungakuchititseninso kusiya utumiki wanu, kumene kungakhale kutaya mwayi waukulu.” Wokamba nkhaniyo anakumbutsa ophunzirawo kuti masiku ano Yesu ndi amene akutsogolera ntchito yokolola mwauzimu ndipo akhoza kuchita chilichonse chimene akufuna kwa otsatira ake. Ngati Yehova ndi Yesu asankha kuchitira anthu ena zabwino kuposa inuyo, sanakulakwireni. Maganizo anu azingokhala pa zinthu zimene Mulungu wakupatsani, ndipo musalole “malipiro” a anthu ena kuti akusokonezeni maganizo pa ntchito imene Yehova wakupatsani.

Zokumana Nazo Komanso Kucheza ndi Ophunzira

Ophunzira a m’sukulu ya Gileadi akakhala kuti sali m’kalasi kapena sakukonzekera maphunziro awo, amapita ku mipingo ya Mboni za Yehova kuti akagwire nawo ntchito yolalikira. Sam Roberson, mmodzi wa alangizi a sukuluyi anafunsa ena mwa ophunzirawo kuti afotokoze zimene anakumana nazo mu utumiki. Mwachitsanzo, mlongo Alessandra Kirchler anakumana ndi mayi wina amene ankadera nkhawa kwambiri mwana wake amene amasuta fodya. Nthawi ina Alessandra anapitanso kwa mayiyo ndi magazini ya Galamukani! imene inali ndi nkhani yokhudza kusuta. Ngakhale kuti sanapeze munthu, iye anasiyabe magaziniyo. Tsiku lina Alessandra anapeza mayiyo pakhomo ndipo anam’landira. Mayiyo anasangalala kwambiri ndi nkhaniyo ndipo ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimafuna kudziwa kuti Mulungu akufuna kundiphunzitsa chiyani ndi mayesero amene ndikukumana nawowa.” Alessandra anamuonetsa zimene Baibulo limanena, kuti Mulungu si amene amachititsa kuti tizikumana ndi mavuto. (Yakobe 1:13) Panopa mayiyu ndi mwana wakeyo akuphunzira Baibulo.

Melvin Jones wa mu Dipatimenti ya Utumiki anafunsa anthu atatu amene kale anachita nawo maphunziro a Gileadi. Anthuwa ndi Jon Sommerud, amene akutumikira ku Albania, Mark Anderson amene akutumikira ku Kenya ndi James Hinderer amene akutumikira mu Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu za Utumiki wa Mulungu. * Anthu onsewa anavomereza kuti sukulu ya Gileadi simangophunzitsa mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo koma imaphunzitsanso mmene angagwiritsire ntchito mfundozo, kaya ophunzirawo ndi ndani kapena akutumikira kuti.

Kenako, mmodzi wa ophunzirawo anawerenga kalata yabwino kwambiri yothokoza chifukwa cha maphunzirowo. John Barr, wazaka 96 amenenso ndi wachikulire kwambiri m’Bungwe Lolamulira, anatseka mwambowu ndi pemphero. M’pempheroli anapempha Yehova kuti adalitse ntchito imene ophunzirawa azikagwira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 22 Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu za Utumiki wa Mulungu imayang’anira sukulu ya Gileadi, sukulu ya Makomiti a Nthambi, ndi sukulu ya oyang’anira oyendayenda.

[Tchati/​Mapu patsamba 31]

ZA OPHUNZIRAWO

8 mayiko amene ophunzira achokera

54 ophunzira

27 mabanja

35.2 avereji ya zaka zakubadwa

19.1 avereji ya zaka zimene akhala Mboni kuchokera pamene anabatizidwa

13.8 Avereji ya zaka zimene akhala akuchita utumiki wa nthawi zonse

[Mapu]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Ophunzirawa anatumizidwa kumayiko 25 amene ali pansipa:

KUMENE AMISHONALE ANATUMIZIDWA

ALBANIA

ARUBA

BOLIVIA

CAMBODIA

CÔTE D’IVOIRE

DOMINICAN REPUBLIC

ECUADOR

GHANA

GUATEMALA

GUINEA

GUYANA

HONDURAS

INDONESIA

KOSOVO

LATVIA

LIBERIA

MADAGASCAR

MONGOLIA

NAMIBIA

NICARAGUA

PARAGUAY

ROMANIA

RWANDA

SERBIA

TAIWAN

(ENA ANATUMIZIDWA KUDERA LINA LOYANG’ANIRIDWA NDI NTHAMBI YA AUSTRALIA)

[Chithunzi patsamba 30]

Ophunzira akusonyeza zimene anakumana nazo mu utumiki

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu la Nambala 128 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pamndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse mayina tawandandalika kuyambira dzina la munthu amene ali kumanzere kupita kumanja.

(1) Keller, E.; Ostopowich, I.; Jacobsen, S.; Arias, M.; Dieckmann, Y.; Tanaka, J.; Harada, K.

(2) Camacho, L.; Kirchler, A.; Rodríguez, S.; Ward, B.; Trenalone, K.; Victoria, V.; Oxley, F.; Nguyen, K.

(3) Oxley, O.; De Dios, A.; Lindström, C.; Allen, J.; Meads, T.; Waddington, J.; Victoria, E.

(4) Harada, H.; Lindström, A.; Orsini, E.; Logue, D.; Missud, T.; Bergeron, S.; Camacho, G.; Ward, T.

(5) Kirchler, W.; Nguyen, H.; Kremer, E.; Burgaud, C.; Titmas, N.; De Dios, C.; Rodríguez, A.; Waddington, M.

(6) Dieckmann, J.; Allen, C.; Titmas, R.; Arias, J.; Bergeron, E.; Keller, J.; Ostopowich, F.; Burgaud, F.

(7) Tanaka, K.; Kremer, J.; Jacobsen, R.; Trenalone, J.; Logue, J.; Meads, D.; Missud, D.; Orsini, A.