Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

6 Kodi Kupemphera N’kothandiza?

6 Kodi Kupemphera N’kothandiza?

KODI kupemphera kungatithandize? Inde, chifukwa Baibulo limanena kuti mapemphero a atumiki okhulupirika a Mulungu amawathandizadi. (Luka 22:40; Yakobo 5:13) Ndipotu, kupemphera kungatithandize kwambiri pa zinthu zauzimu. Kungatithandizenso kuti maganizo athu akhale m’malo ndiponso kuti tikhale ndi thanzi labwino. Kodi zimenezi zingachitike bwanji?

Tiyerekeze kuti muli ndi mwana wamng’ono amene wapatsidwa mphatso. Kodi mungamuphunzitse kuti azingoyamikira mphatsoyo chamumtima? Kapena mungamuphunzitse kuti azinena mawu osonyeza kuti akuyamikira? Tikauza munthu wina mmene tikumvera mumtima mwathu pa nkhani inayake yofunika, timayamba kuganizira kwambiri za nkhaniyo ndipo imakhazikika mumtima mwathu. Kodi zimenezi zimachitikanso tikamalankhula ndi Mulungu? Inde. Taganizirani zitsanzo izi.

Mapemphero oyamikira. Kuyamikira Atate wathu pa zabwino zimene zatichitikira, kumachititsa kuti tiziganizira zinthu zabwino zimene iye amatichitira. Zimenezi zingachititse kuti tikhale ndi mtima woyamikira, tizisangalala komanso tisamangokhalira kudandaula nthawi zonse.​—Afilipi 4:6.

Chitsanzo: Yesu anayamikira Atate wake chifukwa cha mmene ankayankhira mapemphero ake.​—Yohane 11:41.

Mapemphero opempha kuti Mulungu atikhululukire. Tikapempha Mulungu kuti atikhululukire, timakhala ndi chikumbumtima chabwino, timalapadi mochokera pansi pamtima ndipo timazindikira kuopsa kwa zimene tinachitazo. Timapezanso mtendere wa mumtima m’malo mokhala munthu wachisoni.

Chitsanzo: Davide anapemphera posonyeza kulapa ndiponso chisoni chimene anali nacho.​—Salimo 51.

Kupemphera kuti Mulungu atitsogolere ndiponso atipatse nzeru. Kupempha Yehova kuti atitsogolere kapena kuti atipatse nzeru zotithandiza kusankha bwino zochita, kungatithandize kukhala odzichepetsa zenizeni. Kungatikumbutse kuti pali zina zimene sitingathe kuchita ndipo kungatithandizenso kuti tizikhulupirira kwambiri Atate wathu wakumwamba.​—Miyambo 3:5, 6.

Chitsanzo: Solomo anapemphera modzichepetsa kuti Mulungu amutsogolere komanso kuti amupatse nzeru zomuthandiza kulamulira Aisiraeli.​—1 Mafumu 3:5-12.

Kupemphera tikakhala pa mavuto. Tikamutulira Mulungu nkhawa zathu zonse timapeza mtendere wa mumtima ndipo tidzayamba kudalira kwambiri Yehova, m’malo modzidalira tokha.​—Salimo 62:8.

Chitsanzo: Mfumu Asa anapemphera ataopsezedwa ndi mdani wamphamvu kwambiri.​—2 Mbiri 14:11.

Kupempherera ena. Kupempherera ena kumatithandiza kupewa kudzikonda ndipo kumatithandiza kukulitsa mtima wachifundo ndi woganizira ena.

Chitsanzo: Yesu anapempherera otsatira ake.​—Yohane 17:9-17.

Mapemphero otamanda Mulungu. Tikamatamanda Yehova chifukwa cha zinthu zosangalatsa zimene analenga ndiponso makhalidwe ake ochititsa chidwi timayamba kumupatsa ulemu komanso kumuyamikira kwambiri. Mapemphero amenewo angatithandizenso kuti tiyandikire Mulungu, Atate wathu.

Chitsanzo: Davide anatamanda Mulungu ndi mtima wonse chifukwa cha zimene analenga.​—Salimo 8.

Ubwino wina wa pemphero ndi wakuti, timapeza “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:7) M’dziko lamavutoli, n’zosowa kupeza mtendere woterewu. Mtendere wa mumtima umachititsanso kuti tikhale ndi thanzi labwino. (Miyambo 14:30) Komabe kodi mtendere umenewu tingaupeze chifukwa cha khama lathu lokha? Kapena palinso chinthu china chofunika kwambiri?

Pemphero limatithandiza kuti tikhale ndi thanzi labwino, kuti maganizo athu akhale m’malo komanso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu