Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Aramagedo

Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Aramagedo

Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Aramagedo

“Mauthenga ouziridwa ndi ziwanda . . . akupita kwa mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, . . .  Ndipo anawasonkhanitsa pamodzi, kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.”​—CHIVUMBULUTSO 16:14, 16.

MAWU akuti Aramagedo, kapena kuti “Haramagedo,” amanena za malo. Komabe sikuti padziko lapansili pali malo enieni amene amatchedwa Aramagedo.

Kodi mawu akuti “Aramagedo” ndi ofunika chifukwa chiyani? Nanga n’chifukwa chiyani mawu amenewa nthawi zambiri amatchulidwa ponena za zinthu monga nkhondo?

Anawasonkhanitsa Kumalo Otchedwa Aramagedo

Mawu achiheberi akuti Har–​Magedon amatanthauza “Phiri la Megido.” Ngakhale kuti kulibe phiri lotchedwa Megido, malo otchedwa Megido alipo ndithu. Malo amenewa ali pamphambano inayake imene ili kumpoto chakumadzulo kwa dera lina limene Aisiraeli akale ankakhala. Nkhondo zambiri zinkachitikira pafupi ndi malo amenewa. Choncho, mawu akuti Megido anayamba kugwiritsidwa ntchito ponena za nkhondo. *

Komabe malo a Megido ndi ofunika osati chifukwa cha nkhondo zimene zinachitikira pamalopo koma chifukwa chake nkhondozo zinachitika. Dera la Megido linali mbali ya Dziko Lolonjezedwa limene Yehova Mulungu anapatsa Aisiraeli. (Ekisodo 33:1; Yoswa 12:7, 21) Iye analonjeza Aisiraeli kuti adzawateteza kwa adani awo ndipo anaterodi. (Deuteronomo 6:18, 19) Mwachitsanzo, pa Megido m’pamene Yehova anateteza Aisiraeli mozizwitsa kwa magulu ankhondo a mfumu yachikanani dzina lake Yabini limodzi ndi Sisera, yemwe anali mkulu wa gulu lankhondo.​—Oweruza 4:14-16.

Choncho, mawu akuti “Haramagedo,” kapena kuti “Aramagedo,” ali ndi tanthauzo lalikulu ndipo ndi ophiphiritsa. Mawuwa amanena za nkhondo ya pakati pa magulu awiri amphamvu.

Ulosi womwe uli m’buku la Chivumbulutso umanena kuti posachedwapa Satana ndi ziwanda zake achititsa maboma a anthu kusonkhanitsa magulu awo ankhondo. Maboma a anthuwa adzachita zimenezi n’cholinga choti alimbane ndi anthu a Mulungu. Zotsatira zake zidzakhala zoti anthu mamiliyoni ambiri adzafa chifukwa Mulungu adzalowererapo kuti ateteze anthu ake kwa adani awowa.​—Chivumbulutso 19:11-18.

Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu, yemwe Baibulo limanena kuti ndi “wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha,” adzawononge anthu ambiri chonchi? (Nehemiya 9:17) Kuti timvetse chifukwa chake adzachite zimenezi, tiyenera kupeza mayankho a mafunso atatu awa: (1) Kodi ndani adzayambitse nkhondoyi? (2) Kodi Mulungu adzalowerera chifukwa chiyani? (3) Kodi zotsatira za nkhondoyi zidzakhala zotani, ndipo zidzakhudza bwanji anthu okhala padziko lapansi?

1. KODI NDANI ADZAYAMBITSE NKHONDOYI?

Sikuti Mulungu ndi amene adzayambitse Aramagedo chifukwa chokwiya. M’malomwake anthu ndi amene adzaiyambitse, ndipo Mulungu adzalowerera kuti ateteze anthu ake. Amene adzayambitse nkhondoyi ndi “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” kapena kuti atsogoleri a mayiko. Kodi n’chifukwa chiyani iwo adzayambitse nkhondo? N’chifukwa chakuti Satana adzachititsa kuti iwowo komanso magulu ankhondo aukire koopsa anthu amene amalambira Yehova Mulungu.​—Chivumbulutso 16:13, 14; 19:17, 18.

Masiku ano, mayiko ambiri akulimbikitsa ufulu wolankhula komanso wachipembedzo. Choncho, anthu ambiri angaone kuti mfundo yoti maboma adzaukira kapena adzafuna kuthetseratu gulu lililonse la chipembedzo, ndi yosamveka. Koma dziwani kuti zimenezi zinachitikapo kale m’zaka za m’ma 1900 ndipo zikuchitikanso m’mayiko ena panopa. * Komabe padzakhala kusiyana pakati pa zimene zakhala zikuchitika zokhudza kuukiridwa kwa anthu a Mulungu, ndi zimene zidzachitike pa nthawi ya Aramagedo. Choyamba pa nthawi imeneyi anthu a Mulungu padziko lonse lapansi adzaukiridwa. Chachiwiri, zimene Yehova Mulungu adzachite pa nthawiyo ndi zoti sanachitepo m’mbuyo monsemu. (Yeremiya 25:32, 33) Baibulo limanena kuti imeneyi idzakhala ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’

2. KODI MULUNGU ADZALOWERERA CHIFUKWA CHIYANI?

Yehova amauza anthu amene amamulambira kuti azikhala amtendere komanso azikonda adani awo. (Mika 4:1-3; Mateyu 5:43, 44; 26:52) Choncho anthu a Mulungu akadzaukiridwa, sadzamenya nkhondo n’cholinga choti adziteteze. Ngati Mulungu sadzalowerera nkhondoyi, ndiye kuti anthu ake onse adzawonongedwa. Zimenezi zitachitika, zingachititse kuti anthu anyoze Yehova Mulungu ndiponso dzina lake. Komanso ngati anthu a Mulungu onse atafafanizidwa, zingaoneke ngati Yehova ndi wopanda chikondi, chilungamo komanso mphamvu. Choncho, Yehova sangalole kuti zimenezi zichitike.​—Salimo 37:28, 29.

Mulungu safuna kuwononga wina aliyense, choncho akuchenjezeratu anthu za zimene adzachite. (2 Petulo 3:9) Kudzera mu nkhani zimene zili m’Baibulo, iye amatiuza kuti m’mbuyomu anapha anthu amene anaukira anthu ake. (2 Mafumu 19:35) Baibulo limatiuzanso kuti posachedwapa, Satana akadzagwiritsa ntchito anthu ake kuukira anthu a Mulungu, Yehova adzalowererapo ndipo adzamenyana nawo. Ndipotu Baibulo linalosera kalekale kuti Yehova adzawononga anthu oipa. (Miyambo 2:21, 22; 2 Atesalonika 1:6-9) Pa nthawi imeneyo anthu oukirawo adzadziwa kuti akumenyana ndi Mulungu Wamphamvuyonse.​—Ezekieli 38:21-23.

3. KODI ZOTSATIRA ZA NKHONDOYI ZIDZAKHALA ZOTANI?

Pa nkhondo ya Aramagedo, Mulungu adzapulumutsa anthu mamiliyoni ambiri. Ndipotu chimenechi chidzakhala chiyambi cha mtendere wapadziko lonse.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Buku la Chivumbulutso limanena za “khamu lalikulu la anthu” limene lidzapulumuke nkhondo imeneyi. (Chivumbulutso 7:9, 14) Motsogoleredwa ndi Mulungu, anthu amenewa adzathandiza kuti dziko lapansi likhalenso Paradaiso monga mmene Yehova anafunira poyamba.

Kodi ndi liti pamene anthu a Mulungu adzaukiridwe?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Anthu ambiri amagwiritsa ntchito dzina la malo ponena za nkhondo. Mwachitsanzo, mzinda wina wa ku Japan wotchedwa Hiroshima, womwe unawonongedwa ndi bomba, panopa umaonedwa ngati chizindikiro chakuti nkhondo ya zida zoopsa ikhoza kuyambika.

^ ndime 13 Kuphedwa kwa anthu ambiri pa nthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany, ndi chitsanzo cha zimene boma lina linachita pofuna kuthetsa zipembedzo komanso mitundu ina ya anthu. M’nthawi ya ulamuliro wa Soviet Union, magulu azipembedzo omwe anali m’dzikolo ankachitiridwa nkhanza zoopsa. Onani nkhani yakuti, “Anthu Okonda Mtendere Akuyesetsa Kuti Anthu Asaipitse Mbiri Yawo,” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2011, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 6]

Yehova Mulungu anatetezapo anthu ake

[Chithunzi patsamba 7]

Yehova adzatetezanso anthu ake pa nkhondo ya Aramagedo