Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’kulakwa Kukhulupirira Zamizimu?

Kodi N’kulakwa Kukhulupirira Zamizimu?

Kodi N’kulakwa Kukhulupirira Zamizimu?

Mayi wina, dzina lake Barbara, * kuyambira ali mtsikana ankaona masomphenya, kumva mawu achilendo komanso ankakhulupirira kuti ankatha kulankhula ndi achibale ake amene anamwalira. Iye ndi mwamuna wake, dzina lake Joachim, ankakonda kuwerenga mabuku azamatsenga ndipo anakhala akatswiri oombeza pogwiritsa ntchito makadi enaake. Iwo anadziwa kuti zimenezi zikhoza kuwabweretsera ndalama zambiri ndipo ankapangadi ndalama zambiri pa ntchito yawoyi. Koma tsiku lina, kudzera m’makadiwa, iwo anauzidwa kuti kunyumba kwawo kufika anthu oopsa kwambiri ndipo anauzidwanso mmene angadzitetezere.

NGAKHALE kuti kukhulupirira zamizimu kumaoneka kwachikale, anthu ambiri amachita chidwi ndi nkhani zimenezi. Komanso padziko lonse anthu amavala zithumwa, amagwiritsa ntchito matabwa azamatsenga komanso amapita kwa asing’anga kukaombeza kapena kukadziteteza kuti zinthu zoipa zisawachitikire. Nkhani imene inatuluka m’magazini ina ya ku Germany inanena kuti: “Intaneti ikuchititsa kuti anthu azikhala ndi chidwi kwambiri ndi zamatsenga komanso zaufiti.”​—Focus.

Kodi mukudziwa zimene Baibulo limanena pa nkhani yokhudza zamizimu? Mwina mungadabwe mutadziwa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

Zimene Baibulo Limanena Zokhudza Zamizimu

Mulungu anapereka lamulo ili kwa Aisiraeli akale omwe anali anthu ake: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa. Pakuti aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deuteronomo 18:10-12) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anapereka lamulo lamphamvu limeneli pa nkhani ya zamizimu?

Chitsanzo cha Barbara chimene tafotokoza koyamba chija, chikusonyeza kuti anthu ambiri amakhulupirira kuti anthu angathe kulankhula ndi akufa komanso kuti akufawo amathandiza anthu okhulupirira mizimu kuti azitha kudziwa zinthu. Zikhulupiriro zoterezi zimachokera pa zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa zoti munthu akafa, amakakhala ndi moyo kudziko lamizimu. Koma Baibulo siliphunzitsa zimenezi. Ilo limanena momveka bwino kuti: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Baibulo limanena kuti munthu akafa amakhala ngati wagona tulo tofa nato ndipo sadziwa chilichonse chimene chikuchitika. * (Mateyu 9:18, 24; Yohane 11:11-14) Mwina mungafunse kuti, ndiye ngati zili choncho, kodi anthu amene amati alankhula ndi anthu akufa, amakhala atalankhula ndi ndani?

Kulankhulana Ndi Mizimu

Mauthenga Abwino amasonyeza kuti pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi analankhula ndi mizimu. Lemba la Maliko 1:23, 24 limanena kuti “mzimu wonyansa” unauza Yesu kuti: “Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri.” Choncho mizimu iyenera kuti nanunso ikukudziwani. Koma kodi inuyo mumaidziwa?

Mulungu asanalenge anthu, analenga ana ake, kapena kuti angelo ambirimbiri. (Yobu 38:4-7) Koma angelo ndi osiyana ndi anthu. (Aheberi 2:6, 7) Angelo analengedwa kuti azichita chifuniro cha Mulungu ndipo ndi amphamvu komanso anzeru kuposa anthu. Munthu wina amene analemba nawo masalimo anaimba kuti: “Tamandani Yehova, inu angelo ake amphamvu, ochita zimene wanena.”​—Salimo 103:20.

Baibulo limasonyeza kuti patapita nthawi angelo ena anayamba kulankhulana ndi anthu koma Mulungu sanawatume kuti achite zimenezi. Kodi angelowa anachita zimenezi chifukwa chiyani? Mngelo woyamba kuchita zimenezi ananyenga anthu awiri oyambirira, Adamu ndi Hava, ndipo anawachititsa kuti asamvere Mulungu yemwe anali Mlengi wawo. Chifukwa cha zimene anachitazi, iye anadzipangitsa kukhala Satana Mdyerekezi, woneneza komanso wotsutsa Mulungu.​—Genesis 3:1-6.

Kenako angelo enanso “anasiya malo awo okhala” kumwamba n’kuvala matupi a anthu ndipo anakwatira akazi okongola a padziko lapansi. (Yuda 6; Genesis 6:1, 2) Angelo opanduka amenewa komanso ana amene anabereka ankachitira anthu nkhanza moti dziko lonse “linadzaza ndi chiwawa.” Mwina mukudziwa nkhani ya m’Baibulo imene imanena kuti Mulungu anawononga anthu oipa ndi Chigumula m’nthawi ya Nowa.​—Genesis 6:3, 4, 11-13.

Pothawa Chigumulacho, angelo oipawo anavula matupi a anthu ndipo anabwerera kumwamba. Koma Mulungu sanawalole kuti akhalenso ‘pamalo’ awo ndipo anawapatsa chilango chofanana ndi kuwaponya “m’maenje a mdima wandiweyani.” (2 Petulo 2:4, 5) Baibulo limanena kuti angelo opanduka amenewa ndi “ziwanda.” (Yakobo 2:19) Choncho, zinthu zonse zokhudzana ndi zamizimu zimachokera kwa ziwanda zimenezi.

Kodi Cholinga cha Ziwanda N’chiyani?

Cholinga cha ziwanda polankhula ndi anthu n’kufuna kusocheretsa anthuwo kuti asamalambire Yehova, yemwe ndi Mulungu woona. Mphatso kapena mphamvu zimene anthu amene amachita zamizimu amakhala nazo, ndi njira zimene Satana amagwiritsa ntchito pofuna kuwalepheretsa kuti asaphunzire zoona zokhudza Mulungu komanso kuti asakhale naye pa ubwenzi.

Cholinga china cha ziwanda chimaonekera pa zimene mtsogoleri wawo, Satana, anauza Yesu pamene ankamuyesa. Satana anauza Yesu kuti amupatsa “maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo.” Kodi Satana ankafuna kuti Yesu achite chiyani asanamupatse zinthu zimenezi? Iye anauza Yesu kuti: ‘Mungogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.’ Apatu zikuonekeratu kuti Satana ndi ziwanda amafuna kulambiridwa. Koma Yesu ankadziwa kuti Mulungu yekha ndiye woyenera kumulambira choncho anakana kuchita zimenezi.​—Mateyu 4:8-10.

Masiku ano, ziwanda siziuza anthu mwachindunji kuti azilambire. Koma zimasocheretsa anthu pogwiritsa ntchito zinthu zimene zimaoneka ngati zilibe vuto lililonse, monga kuombeza, kukhulupirira asing’anga, kulankhula ndi mizimu ya akufa komanso kukhulupirira nyenyezi. Musalole kuti ziwanda zikusocheretseni. Zinthu zimenezi sizingakuthandizeni kulankhula ndi anthu amene ali kudziko lamizimu. Ziwanda zimakopa anthu pogwiritsa ntchito zamizimu n’cholinga chofuna kuwalepheretsa kuti asamalambire Yehova. Zikalephera kukwaniritsa cholinga chawochi, nthawi zambiri ziwanda zimaukira anthuwo ndipo zimayamba kuwazunza. Ngati zimenezi zakuchitikirani, kodi mungatani kuti musiye kuzikhulupirira?

Zimene Mungachite Kuti Musiye Kukhulupirira Zamizimu

Musapusitsike, ziwanda ndi adani a Mulungu ndipo zikudikira chiwonongeko. (Yuda 6) Ziwanda n’zabodza ndipo zimalankhula ndi anthu n’cholinga chakuti anthuwo aziganiza kuti akulankhulawo ndi anthu amene anamwalira. Kodi mungamve bwanji mutazindikira kuti munthu amene mumam’tenga kuti ndi mnzanu, ndi wachinyengo ndipo akungofuna kukulepheretsani kupeza zinthu zabwino? Nanga mungatani mutazindikira kuti munthu amene mwakhala mukucheza naye pa Intaneti ndi chidyamakanda chimene cholinga chake n’kunyengerera anthu kuti azichita nacho zachiwerewere? Komatu dziwani kuti kugwirizana ndi ziwanda n’koopsa kwambiri kuposa zimenezi, choncho muyenera kusiya chilichonse chokhudzana ndi ziwanda. Koma kodi mungachite bwanji zimenezi?

Anthu a ku Efeso wakale ataphunzira zimene Malemba amanena zokhudza kukhulupirira mizimu, anaona kuti m’pofunika kuwononga mabuku awo azamatsenga ngakhale kuti anali a ndalama zambiri. Iwo ‘anatentha mabukuwo pamaso pa onse.’ (Machitidwe 19:19, 20) Masiku ano anthu ochita zamatsenga amagwiritsa ntchito zinthu ngati mabuku, zithumwa, kuombeza komanso Intaneti. Choncho, muyenera kupewa chilichonse chogwirizana ndi zamatsenga.

Banja limene tatchula koyambirira kwa nkhani ino lija, tsiku lina kudzera m’makadi awo oombezera anaona kuti kunyumba kwawo kufika anthu awiri oopsa. Iwo anaona kuti sayenera kumvetsera zimene anthuwo anene kapena kulandira chilichonse chimene angawapatse. Koma pamene azimayi awiri a Mboni za Yehova, Connie ndi Gudrun, anafika panyumba pawo n’kuwauza kuti awabweretsera uthenga wabwino wonena za Mulungu, Joachim ndi Barbara anaganiza zomvetsera uthengawo. Zina zimene anakambirana zinali zokhudza kukhulupirira mizimu, ndipo Connie ndi Gudrun anawauza zimene Malemba amanena pa nkhaniyi. Joachim ndi Barbara anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

Pasanapite nthawi yaitali, Joachim ndi Barbara, anaganiza zosiya kulankhula ndi ziwanda. A Mboni aja anauza banjali kuti likhoza kuvutitsidwa ndi ziwanda likasiya kuzikhulupirira. Zimenezi zinachitikadi chifukwa Joachim ndi Barbara anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ziwandazo zinkawaopseza komanso kuwachitira zinthu zina zoipa moti kwa nthawi ndithu, iwo ankagona mwamantha mpaka pamene anasamuka m’nyumba yomwe ankakhala. Pa nthawi yonse imene zinthu zimenezi zinkawachitikira, Joachim ndi Barbara ankalimbikitsidwa ndi mawu a palemba la Afilipi 4:13, omwe amati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” Yehova anawadalitsa chifukwa cha kulimba mtima kwawo ndipo patapita nthawi ziwanda zinasiya kuwavutitsa. Panopa, Joachim ndi Barbara ndi osangalala ndipo amalambira Yehova yemwe ndi Mulungu woona.

Baibulo limanena zimene anthu onse angachite kuti alandire madalitso a Yehova. Limati: “Gonjerani Mulungu, koma tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani. Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:7, 8) Ngati mukufuna kusiya kuchita chilichonse chokhudza kukhulupirira zamizimu, Yehova Mulungu ndi wokonzeka kukuthandizani. Joachim ndi Barbara akaganizira mmene Yehova wawathandizira kuti asiye kuchita zamizimu, amavomereza ndi mtima wonse kuti mawu a palemba la Salimo 121:2 ndi oona. Lembali limati: “Thandizo langa lichokera kwa Yehova.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina tawasintha.

^ ndime 7 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene akufa alili, werengani mutu 6 wakuti, “Kodi Akufa Ali Kuti?” m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

Kuchita zamizimu kumalepheretsa anthu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu

[Mawu Otsindika patsamba 22]

“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”​—YAKOBO 4:8