Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chidzachitikire Zipembedzo?

Kodi N’chiyani Chidzachitikire Zipembedzo?

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi N’chiyani Chidzachitikire Zipembedzo?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi zipembedzo zonse n’zabwino?

M’zipembedzo zambiri muli anthu oona mtima amene amafuna kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Mulungu amawaona anthu amenewa ndipo amawadera nkhawa. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amagwiritsa ntchito chipembedzo pofuna kukwaniritsa zolinga zawo zoipa. Kale, atsogoleri ena a chipembedzo ankazunza kwambiri anthu a zipembedzo zina. (2 Akorinto 4:3, 4; 11:13-15) Malinga ndi zimene nyuzipepala zina zinalemba, masiku anonso atsogoleri a chipembedzo ambiri amalimbikitsa uchigawenga kapena nkhondo kapenanso amachitira nkhanza ana.​—Werengani Mateyu 24:3-5, 11, 12.

Baibulo limaphunzitsa kuti zipembedzo zonse zimene zili padzikoli zingagawidwe m’magulu awiri, chipembedzo choona ndi chipembedzo chonyenga. Chipembedzo chonyenga sichiphunzitsa choonadi ponena za Mulungu. Komatu Yehova Mulungu amafuna kuti anthu adziwe zoona zenizeni zokhudza iyeyo.​—Werengani 1 Timoteyo 2:3-5.

2. Kodi n’chiyani chidzachitikire zipembedzo?

Mulungu safuna kuti anthu azisokonezedwa ndi zipembedzo zimene zimanena kuti zimamukonda koma siziphunzitsa choonadi ponena za iye. Ndipotu anthu amene ali m’zipembedzo zimenezi amachita ubwenzi ndi dzikoli limene likulamulidwa ndi Satana Mdyerekezi. (Yakobo 4:4; 1 Yohane 5:19) Mawu a Mulungu amanena kuti zipembedzo zimene zimatumikira maboma a anthu m’malo motumikira Mulungu zili ngati hule. Baibulo limamutchula hule ameneyu kuti “Babulo Wamkulu” ndipo dzina limeneli ndi lochokera ku mzinda wakale kumene chipembedzo chonyenga chinayambira pambuyo pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa. Posachedwapa Mulungu awononga zipembedzo zimene zimasocheretsa komanso kupondereza anthu.​—Werengani Chivumbulutso 17:1, 2, 5, 17; 18:8, 23, 24.

3. Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti anthu onse adzakhale osangalala?

Kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga ndi nkhani yosangalatsa chifukwa kudzachititsa kuti anthu padziko lonse asaponderezedwenso. Zidzachititsanso kuti anthu asasocheretsedwenso kapena kugawikana chifukwa cha chipembedzo. Anthu onse pa nthawiyo adzakhala ogwirizana ndipo azidzalambira Mulungu woona.​—Werengani Yesaya 11:9; Chivumbulutso 18:20, 21; 21:3, 4.

4. Kodi anthu amene amafunadi kusangalatsa Mulungu ayenera kuchita chiyani?

Yehova sanaiwale anthu amene amafunadi kumusangalatsa omwe ali m’zipembedzo zonyenga zosiyanasiyana padziko lonse lapansi. Panopa iye akuthandiza anthu oterewa kuphunzira choonadi n’cholinga choti akhale ogwirizana.​—Werengani Mika 4:2, 5.

Yehova ndi wokonzeka kulandira anthu onse amene akufuna kumutumikira. Ngakhale anzathu kapena achibale athu atakhumudwa chifukwa choti tayamba kutumikira Yehova, timapindula kwambiri. Timakhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso timakhala pa ubwenzi ndi anthu amene amatikonda ndipo amenewa amakhala ngati anthu a m’banja lathu latsopano. Kuwonjezera pamenepa, timakhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha.​—Werengani Maliko 10:29, 30; 2 Akorinto 6:17, 18.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 ndi 16 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

The Complete Encyclopedia of Illustration/​J. G. Heck