Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’koyenera Kumufunsa Mulungu Mafunso?

Kodi N’koyenera Kumufunsa Mulungu Mafunso?

ANTHU ena amanena kuti n’kulakwa kufunsa Mulungu mafunso. Iwo amaganiza kuti n’kupanda ulemu kufunsa Mulungu chifukwa chake amalola kapena salola kuti zinthu zinazake zizichitika. Kodi inunso mumaganiza choncho?

Ngati mumaganiza choncho, mwina mungadabwe kudziwa kuti pali anthu ambiri abwino amene anafunsapo Mulungu mafunso. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anafunsa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani oipa amakhalabe ndi moyo, amakalamba komanso amalemera kwambiri?”Yobu 21:7.

Habakuku, yemwe anali mneneri wokhulupirika nayenso anafunsa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mumayang’ana anthu amene amachita zachinyengo, ndipo n’chifukwa chiyani mukupitiriza kukhala chete pamene munthu woipa akumeza munthu amene ndi wolungama kuposa iyeyo?”Habakuku 1:13.

Yesu Khristu anafunsa Mulungu kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”Mateyu 27:46.

Ngati mungawerenge mavesi otsatira pa mavesi amenewa mupeza kuti Yehova * Mulungu sanakwiye chifukwa chofunsidwa mafunso amenewa. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa mmenemu ndi mmene iye alili. Mwachitsanzo, Mulungu sakwiya tikamamupempha kuti atipatse chakudya. Iyetu amatipatsa zimene tapemphazo. (Mateyu 6:11, 33) Iye amatiphunzitsanso zinthu zimene zingatithandize kuti tizikhala ndi maganizo abwino. (Afilipi 4:6, 7) Ndipotu Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.” (Mateyu 7:7) Nkhani imene Yesu ankakamba pa nthawiyi, imasonyeza kuti sankangonena za kupatsidwa zinthu zakuthupi koma ankanenanso za kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri.

Mutapatsidwa mwayi, kodi ndi funso liti pa mafunso otsatirawa limene mungafune kumufunsa Mulungu?

  • Kodi cholinga cha moyo wanga n’chiyani?

  • Kodi chidzandichitikire n’chiyani ndikadzamwalira?

  • N’chifukwa chiyani mumalola kuti ndizivutika?

Popeza “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,” mungadziwe mayankho a Mulungu pa mafunsowa kuchokera m’Baibulo lomwe ndi Mawu ake. (2 Timoteyo 3:16) Tiyeni tione zimene zinachititsa anthu ena kufunsa mafunso ali pamwambawa komanso tiona mayankho a m’Baibulo a mafunsowa.

^ ndime 7 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.