Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa . . .

N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Sachita Nawo Khirisimasi?

N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Sachita Nawo Khirisimasi?

Padziko lonse lapansi pali anthu pafupifupi 2 biliyoni amene pa 25 December paliponse amakondwerera Khirisimasi, pamene anthu osachepera 200 miliyoni amakondwerera kubadwa kwa Yesu pa 7 January. Komabe palinso anthu ena ambirimbiri omwe sachita Khirisimasi. Kodi n’chifukwa chiyani?

Chifukwa china n’chakuti anthu amenewa sali m’zipembedzo zomwe zimati ndi zachikhristu. Ena mwa anthu amenewa ndi Ayuda, Ahindu kapena Ashinto. Komanso anthu ena amene amati kulibe Mulungu, ndi okayikira zoti kuli Mulungu komanso amene satsatira mfundo zachipembedzo, amaona kuti nkhani yonena za kubadwa kwa Yesu ndi nthano chabe.

Komabe pali gulu lina la anthu amene amakhulupirira Yesu koma sachita nawo zikondwerero zokhudza Khirisimasi. Chifukwa chiyani? Iwo amachita zimenezi pa zifukwa zinayi.

Choyamba, sakhulupirira kuti Yesu anabadwa mu December kapena January. Baibulo silitchula deti lenileni limene Yesu anabadwa. Limangonena kuti: “M’dzikomo munalinso abusa amene anali kugonera ku ubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse mosinthana maulonda. Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova anaima chapafupi ndi iwo, ndipo . . . mngeloyo anawauza kuti: ‘. . . Wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye, mumzinda wa Davide.’”—Luka 2:8-11.

Mfundo zosiyanasiyana zimasonyeza kuti Yesu anabadwa chakumayambiriro kwa mwezi wa October pamene abusa ankakadyetsa ziweto zawo kutchire n’kumagonera komweko. Midzi yapafupi ndi Bethlehem, m’miyezi ya December ndi January kumakhala kozizira kwambiri. Choncho kuti ziweto zisafe ndi kuzizira, abusa amafunika kuzilowetsa m’khola.

Chachiwiri, mwambo umene Yesu anauza otsatira ake kuti azichita pomukumbukira ndi wokhudza imfa yake basi, osati kubadwa kwake. (Luka 22:19, 20) Komanso onani kuti Mauthenga Abwino a Maliko ndi Yohane sananene za kubadwa kwa Yesu.

Mwambo umene Yesu anauza otsatira ake kuti azichita pomukumbukira ndi wokhudza imfa yake basi, osati kubadwa kwake

Chachitatu, palibe umboni wosonyeza kuti Akhristu oyambirira ankakondwerera kubadwa kwa Khristu. Koma iwo ankakumbukira imfa yake. (1 Akorinto 11:23-26) Matchalitchi achikhristu anayamba kuchita Khirisimasi pa 25 December patatha zaka 300 kuchokera pamene Yesu anabadwa. Komanso n’zochititsa chidwi kuti m’zaka za m’ma 1650, nyumba ya malamulo ku England inakhazikitsa lamulo loletsa kukondwerera Khirisimasi. Khoti lina lalikulu la ku America linachitanso chimodzimodzi. N’chifukwa chiyani analetsa? Chifukwa chake chikupezeka m’buku lina limene linati: “Palibe umboni wa m’Baibulo kapena wa mbiri yakale umene umasonyeza kuti Yesu anabadwa pa 25 December.” Bukuli linanenanso kuti Apulotesitanti enaake ankaona kuti “Khirisimasi inali chikondwerero chachikunja chimene Akhristu anangochisintha kuti chikhale chikondwerero chachikhristu.”—The Battle for Christmas.

Chachinayi, mmene Khirisimasi inayambira. Khirisimasi inayambira ku Roma ndipo pa tsikuli ankachita chikondwerero cholemekeza mulungu wa zaulimi ndiponso wa dzuwa. Akatswiri achikhalidwe cha anthu, Christian Rätsch ndi Claudia Müller-Ebeling, analemba m’buku lawo lina kuti: “Mofanana ndi miyambo ndiponso zikhulupiriro zimene anthu ankachita Chikhristu chisanayambe, anthu ankachita chikondwerero cha Khirisimasi chaka chilichonse pokumbukira kubwera kwa dzuwa, ndipo kenako anachisintha n’kukhala chikondwerero chokumbukira kubadwa kwa Khristu.—Pagan Christmas.”

Mogwirizana ndi mfundo zinayi zimene tatchula m’nkhaniyi, kodi mwaona chifukwa chimene Akhristu oona sachitira nawo Khirisimasi?