Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi zidzatheka kukhala ndi boma limodzi lolamulira dziko lonse?

Kodi boma lolamulira dziko lonse lidzathandiza bwanji kuti anthu a mitundu yonse azigwirizana? Yesaya 32:1, 17; 54:13

Kodi mukuganiza kuti zinthu zingakhale bwanji patakhala boma limodzi lolamulira dziko lonse lapansi? Masiku ano anthu ambiri ali pa umphawi wadzaoneni, pomwe ena ndi olemera kwambiri. Koma patakhala boma limodzi lolamulira dziko lonse, lingamaonetsetse kuti anthu onse ali ndi zimene amafunikira. Kodi mukuganiza kuti anthu angathe kukhazikitsa boma loterolo?Werengani Yeremiya 10:23.

Kuyambira kale, maboma akhala akulephera kuthandiza nzika zawo, makamaka anthu osauka. Komanso maboma ena amapondereza anthu awo. (Mlaliki 4:1; 8:9) Koma Mulungu Wamphamvuyonse watilonjeza kuti adzakhazikitsa boma limene lidzalowe m’malo mwa maboma onse. Wolamulira wa boma, kapena kuti Ufumu umenewu, adzaonetsetsa kuti nzika zake zonse zili ndi zofunikira.Werengani Yesaya 11:4; Danieli 2:44.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?

Yehova Mulungu wasankha Mfumu yoyenera kulamulira dziko lonse yemwe ndi Mwana wake, Yesu. (Luka 1:31-33) Yesu ali padziko lapansi, ankakonda kuthandiza anthu. Choncho akamadzalamulira dziko lonse adzathandizanso anthu a mitundu yonse.Werengani Salimo 72:8, 12-14.

Koma kodi anthu onse angafune kuti Yesu akhale Mfumu yawo? Ayi. Komabe, Yehova ndi woleza mtima. (2 Petulo 3:9) Iye akupereka kwa anthu oterewa mwayi woti aphunzire zokhudza Yesu n’cholinga choti avomereze kuti adzakhale Mfumu yawo. Posachedwapa, Yesu adzachotsa anthu oipa n’kubweretsa mtendere pa dziko lonse.Werengani Mika 4:3, 4.