Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU AMENE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

“Ndinkaganiza kuti pali malo atatu amene anthu amapitako akamwalira. Malowa ndi kumwamba, kuhelo kapena kupuligatoliyo. * Ndinkadziwa kuti sindinali woyenera kupita kumwamba chifukwa sindinkachita zabwino kwambiri ndipo sindinali woipitsitsa moti n’kupita kuhelo. Sindinkadziwanso bwinobwino kuti kupuligatoliyo kumapita anthu otani. Ziphunzitso zonsezi ndinkangozimva kwa anthu koma ndinali ndisanaziwerengepo m’Baibulo.”—Lionel.

“Ndinaphunzitsidwa kuti anthu onse amapita kumwamba akamwalira, koma ndinkakayikira ngati zimenezi zinalidi zoona. Ndinkaganiza kuti munthu akamwalira ndiye kuti zake zathera pamenepo.”—Fernando.

Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti: ‘N’chiyani kwenikweni chimachitika munthu akamwalira? Kodi munthu akamwalira, amakazunzika kwinakwake? Kodi anthu amene anamwalira tidzawaonanso? Nanga tingatsimikize bwanji kuti tidzawaonanso?’ Kuti tipeze mayankho a mafunsowa, tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa. Choyamba, tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa. Kenako tiona zimene Baibulo linalonjeza kuti zidzachitikira anthu amene anamwalira.

Kodi akufa amadziwa chilichonse?

YANKHO LA M’BAIBULO: “Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse. Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika. Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.” *Mlaliki 9:5, 10.

Manda ndi kumalo kumene anthu amakaikidwa akamwalira. Ndipo anthu amene amaikidwa kumeneko sadziwa kapena kuchita chilichonse. Kodi Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, ankaona kuti manda ndi malo ozunzirako anthu akufa? Katundu komanso ana onse a Yobu anatha tsiku limodzi lokha. Kenako iyeyo anatuluka zilonda zowawa thupi lonse. Ndiyeno anapempha Mulungu kuti: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda [“mu helo,” Catholic Douay Version], mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utachoka.” (Yobu 1:13-19; 2:7; 14:13) Popeza kuti pa nthawiyi Yobu anali akuzunzika, sakanapempha Mulungu kuti amupititse kumalo kumene akanazunzika kwambiri ndi moto. Choncho Yobu ankaona kuti kumanda ndi kumalo kumene angakapume.

Palinso nkhani zina zimene zingatithandize kudziwa zimene zimachitika munthu akamwalira. Tingawerenge zomwe zinalembedwa m’Baibulo zokhudza anthu 8 omwe anaukitsidwa.—Onani bokosi lakuti “ Anthu 8 Otchulidwa M’Baibulo Amene Anaukitsidwa.”

Anthuwa ataukitsidwa, palibe ngakhale mmodzi amene anafotokoza kuti anali kumalo achisangalalo kapena ozunzirako anthu akufa. Akanakhala kuti anali kumalo oterewa, n’zosachita kufunsa kuti akanafotokozera anthu za malowa. Komanso zimenezi zikanalembedwa m’Baibulo kuti aliyense adziwe. Komatu palibe lemba lililonse la m’Baibulo lomwe limanena zoterezi. Uwu ndi umboni wakuti anthu 8 omwe anaukitsidwawo analibe choti anganene chifukwa sankadziwa kanthu ndipo zinali ngati anagona tulo tofa nato. Ndipotu nthawi zina Baibulo limayerekezera imfa ndi tulo. Mwachitsanzo, limati Davide ndi Sitefano omwe anali anthu okhulupirika “anagona tulo ta imfa.”—Machitidwe 7:60; 13:36.

N’chiyani chidzachitikire anthu amene anamwalira? Kodi angadzakhalenso ndi moyo?

^ ndime 3 Mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, mawu akuti “Manda” amagwiritsidwa ntchito ponena za mawu achiheberi akuti “Sheol” ndiponso achigiriki akuti “Hades.” Mabaibulo ena amagwiritsa ntchito mawu akuti “helo,” komaMalemba sanena kuti malowa ndi kumene kumapita anthu akufa kuti azikazunzika ndi moto.