Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Panopa Ndimaona Kuti Ndingathe Kuthandiza Ena

Panopa Ndimaona Kuti Ndingathe Kuthandiza Ena
  • CHAKA CHOBADWA: 1981

  • DZIKO: GUATEMALA

  • POYAMBA: NDINAKUMANA NDI MAVUTO AAKULU NDILI MWANA

KALE LANGA:

Ndinabadwira m’tauni ya Acul, yomwe ili m’dera lamapiri chakumadzulo kwa dziko la Guatemala. Makolo anga anali a mfuko la Ixil, ndipo fukoli ndi lochokera mumtundu wa Amaya. Ndimalankhula Chisipanishi komabe ndili mwana ndinkalankhula chinenero china chakumudzi kwathu. Pamene ndinkakula n’kuti ku Guatemala kukuchitika nkhondo yapachiweniweni ndipo inachitika kwa zaka 36. Anthu ambiri a mfuko lathu anafa pankhondoyi.

Ndili ndi zaka 4, mchimwene wanga yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 7, ankaseweretsa bomba ndipo linaphulika mwangozi. Mchimwene wangayo anamwalira ndipo ineyo ndinachita khungu. Patapita nthawi ndinayamba kukhala pasukulu ina ya ana osaona mumzinda wa Guatemala. Kumeneku n’kumene ndinaphunzira kuwerenga zilembo za anthu osaona. Aphunzitsi a pasukuluyi sankandilola kuti ndizicheza ndi anzanga komanso anzangawo ankandisala. Sindinkadziwa kuti ankachitiranji zimenezo. Chaka chilichonse, tinkaloledwa kupita ku holide kwa miyezi iwiri basi. Chifukwa choti ndinkasowa wocheza naye, ndinkalakalaka nditabwerera kunyumba kuti ndikaone mayi anga omwe ankandikonda kwambiri. Ndili ndi zaka 10 zokha, mayi anga anamwalira ndipo ndinamva chisoni kwambiri. Ndinavutika maganizo kwambiri chifukwa ndinaona kuti ndataya munthu wofunika kwambiri pa moyo wanga.

Ndili ndi zaka 11, ndinabwereranso kwathu kumene ndinakayamba kukhala ndi mchimwene wanga wina. Mchimwene wangayu ankandisamalira bwino komabe ndinkavutikabe maganizo. Nthawi zambiri ndinkalira ndipo ndinkapemphera kwa Mulungu kuti ndidziwe kuti n’chifukwa chiyani mayi anga anamwalira komanso chifukwa chake ndili wakhungu. Anthu ena ankandiuza kuti Mulungu ndi amene anakonza zoti ndikumane ndi mavutowa. Zimenezi zinkandipangitsa kuona kuti Mulungu ndi wankhanza kwambiri. Ndinkafuna kudzipha koma njira ndi imene inkandisowa.

Ndinkavutika maganizo kwambiri ndikaganizira zoti ndine wosaona. Komanso ndili wamng’ono, nthawi zambiri anthu ankandichitira zachipongwe komanso kundigwiririra. Sindinkauza aliyense zomwe zinkandichitikirazi chifukwa ndinkaona kuti palibe akanandithandiza. Anthu sankakonda kundilankhula ndipo inenso sindinkalankhula ndi aliyense. Ndinkadzipatula ndipo sindinkakhulupirira aliyense.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Nthawi ina nditatsala pang’ono kukwanitsa zaka 15, kusukulu kwathu kunabwera banja lina la Mboni. Mphunzitsi wathu wina yemwe ankadziwa zomwe ndinkakumana nazo, anauza a Mboniwo kuti adzabwerenso kudzacheza nane. A Mboniwo atabwera anandiuza zimene Baibulo limanena. Anandiphunzitsa kuti akufa adzauka komanso kuti osaona adzayamba kuona. (Yesaya 35:5; Yohane 5:28, 29) Zimene anandiuza zinandigwira mtima, koma sindinathe kufunsa zambiri chifukwa sindinkakonda zolankhula. Komabe, ankabwerabe kudzandiphunzitsa Baibulo. Banjali linkayenda mtunda woposa makilomita 10, kudutsa m’mapiri kuti adzandiphunzitse.

Mchimwene wanga anandiuza mmene anthuwo ankaonekera. Anandiuza kuti amavala bwino ngakhale kuti amaoneka kuti ndi osauka. Komabe ankaoneka kuti amandiganizira moti ankandibweretsera mphatso. Ndinkaona kuti ndi Akhristu enieni okha amene angachite zimenezi.

Pophunzira Baibulo, ndinkagwiritsa ntchito mabuku a anthu osaona. Ndinkamvetsa ndithu zomwe ndinkaphunzira, kungoti panali zinthu zina zomwe zinkandivuta kuvomereza. Mwachitsanzo, zinkandivuta kuvomereza kuti Mulungu amandiganizira komanso zoti pangapezeke anthu ena omwe angandithandizedi kudziwa Mulungu. Ndinamvetsa chifukwa chake Yehova amalola kuti zoipa zizichitika, komabe zinkandivuta kuvomereza kuti Yehova ndi Atate wachikondi. *

Koma m’kupita kwa nthawi, zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kusintha maganizo. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kuti Mulungu sasangalala anthu akamavutika. Pa nthawi ina pamene atumiki ake ankazunzidwa, Mulungu anati: “Ndaona nsautso ya anthu anga . . . ndikudziwa bwino zowawa zawo.” (Ekisodo 3:7) Kenako ndinayamba kuona kuti Yehova ndi Mulungu wabwino kwambiri ndipo ndinaganiza zoti ndidzipereke kwa iye kuti ndizimutumikira. Ndinabatizidwa mu 1998 n’kukhala wa Mboni za Yehova.

Ndili ndi bambo amene ananditenga kuti ndizikhala nawo

Patatha chaka nditabatizidwa, ndinakachita nawo maphunziro a anthu osaona pafupi ndi mzinda wa Escuintla. Akulu a mumpingo wathu anadziwa kuti zikundivuta kuti ndizipita kukasonkhana ndi a Mboni anzanga. Mpingo wapafupi unali kumapiri komwe kunkachokera banja lomwe linkandiphunzitsa lija ndipo kunkanditalikira kwambiri. Choncho akuluwo anapempha banja lina lomwe linkakhala ku Escuintla kuti ndizikakhala nalo n’cholinga choti ndizikapezeka pamisonkhano. Mpaka lero banjali limandisamalirabe ngati mwana wawo weniweni.

Dzuwa likhoza kulowa nditati ndinene zabwino zonse zimene a Mboni anzanga akhala akundichitira. Zimenezi zandithandiza kutsimikizira kuti a Mboni ndi Akhristu oona.—Yohane 13:34, 35.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Panopa sindidzionanso ngati munthu wachabechabe. Ndazindikira kuti pali zinthu zambiri zomwe ndingathe kuchita. Mwachitsanzo, ndimathera nthawi yanga yonse ndikulalikira komanso kuphunzitsa anthu mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamangoganizira za mavuto anga. Komanso ndine mkulu mumpingo wathu moti nthawi zambiri ndimakamba nkhani zochokera m’Baibulo kumpingo kwathu komanso kumipingo ina. Ndimakambanso nkhani pamisonkhano ikuluikulu.

Ndikukamba nkhani pogwiritsa ntchito Baibulo la zilembo za anthu osaona

Mu 2010, ndinalowa nawo Sukulu Yophunzitsa Utumiki (panopa imatchedwa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu) yomwe inachitikira ku El Salvador. Sukuluyi inandithandiza kuti ndizitha kugwira bwino ntchito mumpingo. Inandithandizanso kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi amene akhoza kuphunzitsa aliyense kuti agwire ntchito yake.

Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Poyamba ndinkaona ngati n’zosatheka kukhala wosangalala, koma panopa ndine wosangalala chifukwa ndimathandiza ena.

^ ndime 13 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amalola kuti zoipa zizichitika, onani mutu 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.