Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 121

Timafunika Kukhala Odziletsa

Timafunika Kukhala Odziletsa

(Aroma 7:14-25)

  1. 1. Timakonda Yehova kwambiri

    Koma poti ndife anthu ochimwa,

    Timafunika kudziletsa.

    Mzimu umatithandizadi.

  2. 2. Tsiku ndi tsiku timayesedwa.

    Uchimowu ungatisocheretse

    Koma choonadi n’champhamvu.

    Yehova amatithandiza.

  3. 3. Tilemekeze dzina la M’lungu

    Muzochita ndiponso zolankhula.

    Cholinga chathu chiyenera

    Kukhala anthu odziletsa.