Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 126

Khala Maso, Khala Wolimba, Khala Wamphamvu

Khala Maso, Khala Wolimba, Khala Wamphamvu

(1 Akorinto 16:13)

  1. 1. Khala maso, upirire.

    Ukhalebe wamphamvu.

    Ukhale wolimba mtima,

    Udzapambana ndithu.

    Uzimvera mawu a Yesu.

    Ukhalebe ku mbali yake.

    (KOLASI)

    Khala maso, khala wamphamvu.

    Limba mpaka mapeto.

  2. 2. Khala maso, usagone.

    Ukonzeke kumvera,

    Uzimvera malangizo

    Ochokera kwa Yesu.

    Uzimveranso malangizo

    Omwe akulu akupatsa.

    (KOLASI)

    Khala maso, khala wamphamvu.

    Limba mpaka mapeto.

  3. 3. Tikhale ogwirizana

    Poteteza uthenga.

    Ngakhale tizitsutsidwa

    Tizilalikirabe.

    Timutamande mwachimwemwe.

    Tsiku lake layandikira

    (KOLASI)

    Khala maso, khala wamphamvu.

    Limba mpaka mapeto.