Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 140

Tidzakhala Ndi Moyo Wosatha

Tidzakhala Ndi Moyo Wosatha

(Yohane 3:​16)

  1. 1. Onani m’maganizo,

    Mtendere uli konse,

    Chisoni nacho chatha,

    Kulira kwathanso.

    (KOLASI)

    Tiimbire M’lungu

    Mosangalaladi.

    Patsikulo tidzati,

    ‘Zakale zapita.’

  2. 2. Sitidzakalambanso,

    Tidzakhala ndi mphamvu.

    Mavutowa adzatha,

    Sitidzaliranso.

    (KOLASI)

    Tiimbire M’lungu

    Mosangalaladi.

    Patsikulo tidzati,

    ‘Zakale zapita.’

  3. 3. Tizidzasangalala

    Poimbira Mulungu.

    Tidzamulemekeza

    Mpaka kale kale.

    (KOLASI)

    Tiimbire M’lungu

    Mosangalaladi.

    Patsikulo tidzati,

    ‘Zakale zapita.’