Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 21

Muziika Ufumu Pamalo Oyamba

Muziika Ufumu Pamalo Oyamba

(Mateyu 6:33)

  1. 1. Chinthu chapadera chomwe

    Tikuchidikirira

    Ndi Ufumu wa Mulungu

    Womwe ukonze zonse.

    (KOLASI)

    Muike Ufumu wake

    Poyamba nthawi zonse

    Ndipo muzimutamanda

    Ndi kumutumikira.

  2. 2. Musade nkhawa za mawa,

    Za chakudya ndi madzi.

    Mulungu adzatipatsa

    Zofunikira zonse.

    (KOLASI)

    Muike Ufumu wake

    Poyamba nthawi zonse

    Ndipo muzimutamanda

    Ndi kumutumikira.

  3. 3. Choncho muzilalikira.

    Muzithandiza anthu

    Kuti adalire M’lungu

    Ndi Ufumu wakenso.

    (KOLASI)

    Muike Ufumu wake

    Poyamba nthawi zonse

    Ndipo muzimutamanda

    Ndi kumutumikira.