NYIMBO 30
Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa
-
1. Nthawi zina m’dzikoli
Zinthu zingakhale zovuta.
Komabe ndizingoti
Moyo ndi wabwino.
(KOLASI)
M’lungu ndi wolungama
Sadzaiwala ntchito zanga.
Ali pafupi nane
Nthawi zonse sanditaya.
Iye adzandipatsa
Zonse zomwe ndifunikira.
Ndi Atate, Ndi Mulungu,
Bwenzi langa.
-
2. Panopa ndakalamba.
Tsopano ndi nthawi yovuta
Koma chiyembekezo
Changa ndi champhamvu.
(KOLASI)
M’lungu ndi wolungama
Sadzaiwala ntchito zanga.
Ali pafupi nane
Nthawi zonse sanditaya.
Iye adzandipatsa
Zonse zomwe ndifunikira.
Ndi Atate, Ndi Mulungu,
Bwenzi langa.
(Onaninso Sal. 71:17, 18.)