Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 32

Khalani Kumbali ya Yehova

Khalani Kumbali ya Yehova

(Ekisodo 32:26)

  1. 1. Kalekale tinali mumdima,

    Pokhala m’chipembedzo chabodza.

    Koma pano tikusangalala

    Tadziwa choonadi.

    (KOLASI)

    Khala kumbali ya Yehova M’lungu.

    Ukamamumvera, sangakusiye.

    Lengeza uthenga wamtenderewu.

    Ulamuliro wa M’lungu sudzatha.

  2. 2. Timakhala ku mbali ya M’lungu

    Polalikira kwa anthu onse

    Kuti nawo azisankha okha

    Kumvera M’lungu wathu.

    (KOLASI)

    Khala kumbali ya Yehova M’lungu.

    Ukamamumvera, sangakusiye.

    Lengeza uthenga wamtenderewu.

    Ulamuliro wa M’lungu sudzatha.

  3. 3. Sitidzamuopa Mdyerekezi.

    Tidzakhulupirira Yehova.

    Kaya adani angachuluke,

    M’lungu ndi mphamvu yathu.

    (KOLASI)

    Khala kumbali ya Yehova M’lungu.

    Ukamamumvera, sangakusiye.

    Lengeza uthenga wamtenderewu.

    Ulamuliro wa M’lungu sudzatha.