Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 52

Kudzipereka Monga Mkhristu

Kudzipereka Monga Mkhristu

(Aheberi 10:7, 9)

  1. 1. Yehova Mulungu wathu

    Analenga zonse.

    Dzikoli ndi mlengalenga

    Zonsezi ndi zake.

    Iye watipatsa moyo,

    Wasonyeza kuti

    Ndi woyenera kum’tamanda

    Ndiponso kum’lambira.

  2. 2. Yesu atabatizidwa

    Anauza M’lungu:

    ‘Ndabwera kuti ndichite

    Chifuniro chanu.’

    Mulungu anamudzoza

    Atabatizidwa

    Kuti azimutumikira

    Monga wodzipereka.

  3. 3. Yehova ife tabwera

    Kukutamandani.

    Tadzipereka kwa inu

    Ndipo tadzikana.

    Munatikonda kwambiri

    Potipatsa Yesu.

    Tasiya zomwe timafuna

    Tizichita za inu