Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 75

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

(Yesaya 6:8)

  1. 1. Anthu ena amanyoza

    Dzina loyera la M’lungu.

    Amati ali ndi nkhanza

    Kapena kulibe M‘lungu.

    Ndani akaliyeretse

    Dzina la Yehova M’lungu?

    (KOLASI 1)

    ‘Ndilipo! Nditumizeni.

    Ndikawauza za inu.

    Uwu ndi mwayi waukulu.

    Ine nditumizeni.’

  2. 2. Ena samaopa M’lungu

    Akumati akuchedwa.

    Ena samamulambira

    Amakonda Kaisara.

    Ndani akawachenjeze

    Za nkhondo ya M’lungu wathu?

    (KOLASI 2)

    ‘Ndilipo! Nditumizeni.

    Ine ndikawachenjeza.

    Uwu ndi mwayi waukulu.

    Ine nditumizeni!’

  3. 3. Anthu akudandaula,

    Zoipa zikuchuluka.

    Iwo akufunitsitsa

    Atadziwa choonadi.

    Ndani akawatonthoze?

    Ndani akawathandize?

    (KOLASI 3)

    ‘Ndilipo! Nditumizeni.

    Ndikaphunzitse ofatsa.

    Uwu ndi mwayi waukulu.

    Ine nditumizeni.’

(Onaninso Sal. 10:4; Ezek. 9:4.)