Pitani ku nkhani yake

Kodi Akazi a Chipembedzo Chanu Amalalikira?

Kodi Akazi a Chipembedzo Chanu Amalalikira?

Inde. Munthu aliyense wa Mboni za Yehova, kuphatikizapo akazi ambirimbiri, amalalikira. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu a m’Baibulo akuti “akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”—Salimo 68:11.

Akazi amene ndi a Mboni za Yehova amatsanzira chitsanzo cha akazi otchulidwa m’Baibulo. (Miyambo 31:10-31) Iwo amagwira nawo ntchito yolalikirayi ngakhale kuti sakhala ndi udindo uliwonse mumpingo. Komanso amaphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo. (Miyambo 1:8) Mwa zochita ndi zolankhula zawo, akazi omwe ndi a Mboni amalimbikitsa ena kuti azichita zinthu zabwino.—Tito 2:3-5.