Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sayankha Nkhani Zina Zomwe Anthu Amawanena?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sayankha Nkhani Zina Zomwe Anthu Amawanena?

Baibulo limasonyeza kuti si bwino kumangoyankha pa zilizonse zomwe anthu angatineneze kapena kutinyoza. Choncho a Mboni za Yehova amatsatira malangizo amenewa. Mwachitsanzo mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Amene amalangiza wonyoza amadzichotsera yekha ulemu.” (Miyambo 9:7, 8; 26:4) Ndiyeno m’malo momangodandaula pa nkhani zabodza zomwe anthu amanena, ife timaona kuti chofunika kwambiri n’kuchita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo.​—Salimo 119:69.

Baibulo limati pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:7) Choncho, timayankha anthu amene akufunadi kudziwa zoona, ndipo timapewa mikangano yopanda phindu. Tikamachita zimenezi timakhala tikutsanzira zimene Yesu ndi Akhristu oyambirira ankaphunzitsa.

  • Yesu sanayankhe chilichonse pa nthawi imene anthu ankamunenera zabodza pamaso pa Pilato. (Mateyu 27:11-14; 1 Petulo 2:21-23) Yesu sanayankhenso pamene anamunamizira kuti ndi wosusuka komanso wokonda kumwa kwambiri vinyo. M’malo mwake iye ankachita zinthu zabwino kuti anthu aone okha ntchito zake zabwino. Ndipo zimenezi n’zogwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.” (Mateyu 11:19) Ngakhale zinali choncho, nthawi zina Yesu ankayankha molimba mtima anthu omwe ankamunena zachipongwe.​—Mateyu 15:1-3; Maliko 3:22-30.

    Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti asamakhumudwe ndi nkhani zabodza zimene anthu akuwaneneza. Iye anawauza kuti: “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine.” (Mat. 5:11, 12) Koma anawauzanso kuti ngati mpofunika kuyankha zomwe anthu akunenazo, iye adzakwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Ine ndidzakuuzani mawu oti munene ndi kukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.”​—Luka 21:12-15.

  • Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti azipewa kukangana ndi anthu omwe amangofuna kutsutsana nawo ndipo ananena kuti mikangano yotereyi ndi ‘yosapindulitsa ndiponso yachabechabe.’—Tito 3:9; Aroma 16:17, 18.

  • Mtumwi Petulo analimbikitsa Akhristu kuti azinena zimene amakhulupirira ngati mpofunika kunena. (1 Petulo 3:15) Komabe iye ankadziwa kuti zimene munthu amachita n’zimene zimasonyeza kwambiri zimene amakhulupirira kuposa zimene amanena. Ndipo analemba kuti: “Mwa kuchita zabwino muwatseke pakamwa anthu opanda nzeru olankhula zaumbuli.”—1 Pet. 2:12-15.