Pitani ku nkhani yake

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Philippines Gawo 2 (Kuyambira June 2015 Mpaka June 2016)

Zithunzi Zosonyeza Ntchito Yomanga ku Philippines Gawo 2 (Kuyambira June 2015 Mpaka June 2016)

A Mboni za Yehova ku Philippines, anamaliza ntchito yaikulu yokonza ofesi yawo ya nthambi mumzinda wa Quezon. M’zithunzizi muona mmene ntchitoyi inayendera komanso mmene anthu anadziperekera pogwira ntchitoyi kuyambira mu June 2015 mpaka June 2016. Pambuyo pa miyezi ingapo, ntchito yokonza nyumbazi inatha ndipo mwambo woti nyumbazi zingayambe kugwiritsidwa ntchito unachitika mu February 2017.

Nyumba ndi zinthu zina zomwe zinamangidwa kapena kukonzedwa ndi monga:

  • Nyumba 4 (Yogona)

  • Nyumba 5 (Mojambulira Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera, Dipatimenti Yoona za Utumiki)

  • Nyumba 6 (Dipatimenti Yokonza Kaonekedwe ka Malo, Garaja, Kootchererako Zinthu)

  • Nyumba 7 (Dipatimenti ya Makompyuta, Yazomangamanga, Yokonza Zinthu, Yotumiza Mabuku, Yomasulira Mabuku)

15 June, 2015​—Mu Mzinda wa Quezon

Gulu la anthu oika konkire akukonza chikombole choikira konkire m’njira zoyendamo popita ku Nyumba 1, 5, ndi 7.

June 15, 2015​—Nyumba 5

Asanayambe kugwira ntchito makalipentala akuona kaye pulani yojambulidwa ndi Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga M’mayiko Angapo—Asia/Pacific. Dipatimentiyi inasamuka kuchoka ku Australia kupita ku Philippines mu March 2016.

23 June, 2015​—Mumzinda wa Quezon

Akuphwanya konkire yomwe inali m’njira yodutsa magalimoto kuti ayambe kukumbapo. Akamaliza kukumba, adzaika mapaipi a makina a mpweya woziziritsira nyumba.

20 July, 2015​—Mumzinda wa Quezon

Mwamuna ndi mkazi wake ochokera ku United States akukonza zitsulo zoika m’mbali mwa njira zodutsa anthu.

20 July, 2015​—Mumzinda wa Quezon

Akukwirira mapaipi a madzi ozizira pakati pa Nyumba 4 ndi 5.

18 September, 2015​—Nyumba 5

Kalipentala akumangirira zitsulo m’mawindo.

18 September, 2015​—Nyumba 5

Akuika kalapeti. Mbaliyi yaikidwa kalapeti pofuna kuchepetsa phokoso chifukwa izigwiritsidwa ntchito ndi Dipatimenti Yojambula.

22 October, 2015​—Nyumba 5

Akupaka penti yoteteza nyumba kumphamvu ya dzuwa. Pentiyi imathandiza kuti mkati mwa nyumba mukhale mozizira bwino ndipo zimenezi zimathandiza kuti anthu asamagwiritse ntchito kwambiri makina oziziritsira mpweya.

10 February, 2016​—Nyumba 4

Akuchotsa chikombole choikira konkire mumpanda. Nyumba 4 ndi ya nsanjika ziwiri ndipo ili ndi zipinda zogona ophunzira a sukulu za Baibulo zosiyanasiyana.

10 February, 2016​—Nyumba 4

Akukutira mapaipi a madzi ozizira. Mapaipiwa akawakutira zimathandiza kuti kukamatentha madzi a m’mapaipiwa asatenthe komanso kuti asamachite mame kwambiri.

16 February, 2016​—Nyumba 4

Wogwira ntchito zamagetsi wochokera ku Australia akuyeza switchi yomwe imadula moto wa magetsi ngati chipangizo china chili ndi vuto. Anthu a maluso osiyanasiyana opitirira 100 ochokera m’mayiko ena anapemphedwa kuti adzathandize nawo ntchito yokonza nthambi ya Philippines.