Pitani ku nkhani yake

Amalimbikitsa Ena Ngakhale Kuti Akudwala

Amalimbikitsa Ena Ngakhale Kuti Akudwala

 Mayi wina wa Mboni za Yehova dzina lake Clodean, amakhala ku South Africa ndipo nthawi ina anagonekedwa m’chipatala n’kupangidwa opaleshoni yaikulu. Anamupeza ndi mavuto ambiri m’thupi mwake ndipo panali njira zambiri zomwe zinkafunika kutsatiridwa kuti amuthandize. Asanamuchite opaleshoni komanso pambuyo pake, ankakhala wofooka, ankamva ululu komanso ankapanikizika maganizo. Patatha pafupifupi miyezi iwiri ndi hafu atabwerera kunyumba, ankangokhala chigonere. Zinalinso zovuta kuti anthu ena amuyendere kudzamuona chifukwa cha mliri wa COVID-19.

 Clodean sankafuna kuti azingokhalira kudzimvera chisoni, choncho anapemphera kwa Yehova kuti amupatse mphamvu zoti azitha kulimbikitsa anthu ena. Atangoyamba kukhala pansi, anaimbira foni mayi wina amene ndi mng’ono wawo wa aneba ake. Mayiyo, nthawi ina ankaphunzira Baibulo ndi Amboni koma anasiya. Anakambirana naye mfundo yolimbikitsa ya m’Mawu a Mulungu ndipo anayambiranso kuphunzira Baibulo. Clodean anamufotokozeranso za kufunika kopezeka pamisonkhano yathu komanso anamuthandiza kudziwa zomwe angachite kuti azilumikiza ku misonkhano yampingo yochitikira pa vidiyokomfelensi. Mayi uja anayambadi kupezeka pamisonkhano ndiponso kupereka ndemanga papulogalamu yokambirana ndi omvera.

 Kenako Clodean analankhulanso ndi mng’ono wake wa mayi uja, amenenso ankafuna kuphunzira Baibulo. Iye anauza Clodean za anthu enanso omwe anali ndi chidwi. Ndiye zinatha bwanji? Clodean anayamba kuphunzira Baibulo ndi azimayi enanso 4. Koma sizinathere pomwepo.

Clodean

 Chifukwa choti Clodean ankachita chidwi ndi anthu, anayambanso kuphunzira Baibulo ndi azimayi enanso okwanira 10. Anthu 16 onsewa, anawapeza pa nthawi ya mliriwu. Ena mwa anthuwa amapezeka pamisonkhano nthawi zonse kudzera pa vidiyokomfelensi. Kudzitangwanitsa ndi zinthu zimenezi kwathandiza Clodean kuti asamangokhalira kuganizira za mavuto ake. Iye amaonanso kuti, chifukwa choti Yehova ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” anamutonthoza pamene ankakumana ndi mavuto. Ndipo nayenso anakwanitsa kutonthoza anthu ena.​—2 Akorinto 1:3, 4.

 Kodi anthu omwe ankaphunzira ndi Clodean ananena zotani pa zomwe anaphunzirazo? Mmodzi wa anthuwa ananena kuti: “Ndapindula m’njira zambiri. Koma chachikulu ndi choti ndaphunzira kuti Mulungu ali ndi dzina. Zimenezi zandithandiza kuti ndikhale naye pa ubwenzi.” Mayi woyambirira uja amene Clodean anamuimbira foni, panopa akuyembekezera kubatizidwa. Zochitikazi, zamuthandiza Clodean kuti azikhala wosangalala. Panopo Clodean akupezako bwino.