Pitani ku nkhani yake

DECEMBER 3, 2014
DENMARK

A Mboni za Yehova Athandiza Achipatala Kupanga Opaleshoni Odwala Popanda Kuwapatsa Magazi ku Denmark

A Mboni za Yehova Athandiza Achipatala Kupanga Opaleshoni Odwala Popanda Kuwapatsa Magazi ku Denmark

COPENHAGEN, Denmark—Ofalitsa nkhani ambiri odziwika bwino m’dzikoli ananena kuti m’zipatala za m’chigawo cha Copenhagen, anayamba kupanga anthu opaleshoni popanda kugwiritsa ntchito magazi. Magazini ina inanenanso kuti: “Achipatala atulukira kuti angathe kuthandiza odwala ambiri popanda kupatsidwa magazi. Ndipotu zimenezi zikutheka chifukwa chakuti a Mboni za Yehova sankalola kupatsidwa magazi.” (Kristeligt Dagblad) Padziko lonse pali a Mboni za Yehova opitirira 8,000,000 ndipo m’dziko la Denmark mokha muli a Mboni za Yehova oposa 14,000. Onsewa amakana kupatsidwa magazi chifukwa cha zimene amakhulupilira kuchokera m’Baibulo.

M’zipatala za ku Denmark amagwiritsa ntchito kwambiri magazi kuposa m’zipatala zina zonse za padziko lapansi. Komabe webusaiti ina yofalitsa nkhani yotchedwa Politiken inafalitsa nkhani ina yomwe inanena kuti, “a Mboni za Yehova anapangitsa madokotala kuti apeze njira zina zowonjezera magazi” m’malo moika magazi. Mwachitsanzo, munthu akakhala kuti akufunika kupangidwa opaleshoni, amamupatsa kaye mankhwala owonjezera magazi monga Iron, mavitamini a B complex ndi erythropoietin, yemwe amathandiza kuti maselo ofiira apangike ambiri. Ndipo pa nthawi ya opaleshoni amamupatsanso mankhwala othandiza kuti magazi akhale olimbirako n’cholinga choti asatayike ambiri. Nyuzipepala ina inafotokoza kuti “chaka chilichonse a Mboni za Yehova pafupifupi 10 amachitidwa opaleshoni ya mtima ku chipatala chotchedwa Aarhus University Hospital Skejby” cha ku Denmark popanda kupatsidwa magazi.—The Copenhagen Post.

Chipatala cha Rigshospitalet, chomwe chili ndi akatswiri ambiri azachipatala chomwenso ndi chimodzi mwa malo a maphunziro a zamakhwala ku Denmark chinayamba kupatsa odwala mankhwala ochulukitsa magazi m’chaka cha 2009.

Ogwira ntchito zachipatala ku Denmark azindikira kuti kugwiritsa ntchito magazi pothandiza anthu kumaika moyo wa odwala pangozi. M’chaka cha 2009, chipatala cha Rigshospitalet chomwe chili ku Copenhagen chinayamba kupatsa odwala mankhwala owonjezera magazi. Ndipo nyuzipepala ina inanena kuti zimenezi zachititsa kuti madokotala azithandiza odwala ambiri popanda kuwapatsa magazi komanso kuti odwala ambiri “asamakumane ndi mavuto kapenanso kumwalira.” (Berlingske) Zipatala zambiri za ku Copenhagen zayambanso kugwiritsa ntchito njira imeneyi ndipo zipatala za m’zigawo zina zikufuna ziyambenso kugwiritsa ntchito njira imeneyi.

Nyuzipepalayi inafotokozanso zimene ananena a Dr. Morten Bagge Hansen omwe ndi wofufuza komanso mkulu wa nyumba yosungira magazi ya chipatala (blood bank) cha Rigshospitalet. Iwo ananena kuti zomwe dziko la Denmark linachita poyamba kuthandiza odwala popanda kuwapatsa magazi “ndi zabwino ndipo zikuthandiza kwambiri odwala.” Kuwonjezera pamenepa, siteshoni ya wailesi ya Denmark Radio ndiponso nyuzipepala ya Kristeligt Dagblad inafotokoza zomwe ananena a Dr. Astrid Nørgaard omwe ndi mkulu woona za mankhwala pa chipatala cha Rigshospitalet. Mkuluyu ananena kuti, “popanda a Mboni za Yehova sitikanadziwa kuti n’zotheka kuthandiza odwala popanda kugwiritsa ntchito magazi.”

Kuchokera m’mayiko ena:

Lankhulani ndi: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Denmark: Erik Jørgensen, tel. +45 59 45 60 00