Pitani ku nkhani yake

APRIL 23, 2020
ECUADOR

A Mboni ku Ecuador Akukwanitsa Kulalikira Ali Kunyumba Kwawo

A Mboni ku Ecuador Akukwanitsa Kulalikira Ali Kunyumba Kwawo

Abale ndi alongo athu padziko lonse akuyesetsabe kupeza njira zina zolalikirira pa nthawi yomwe mliri wa COVID-19 ukupitirirabe kufalikira. Ku Ecuador, ofalitsa akugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana kuti alalikire uthenga wabwino ndipo zinthu zikuwayendera bwino.

Mumzinda wa Ambato, wofalitsa wazaka 7 limodzi ndi mayi ake, anatumizira mameseji aziphunzitsi ake akusukulu. M’mameseji ena analembamo kuti: “Mwadzuka bwanji aphunzitsi. Ndalemba kalatayi kuti ndikulimbikitseni m’nthawi yovuta yomwe tikukhalayi. Pa Chivumbulutso 21:4, Baibulo limatilonjeza kuti kutsogoloku zinthu zidzakhala bwino. Ndakutumiziraninso linki yokuthandizani kudziwa zambiri.”

Mphunzitsi wina anayankha kalatayo ponena kuti: “Zikomo kwambiri mtsikana wanga. Ngakhale kuti ndiwe wamng’ono, zomwe walembazi n’zothandiza kwambiri.” Mphunzitsi winanso anamuyamikira n’kumupempha ngati angakhale ndi buku lakuti, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo la pachipangizo chamakono. Mphunzitsiyo ananena kuti poyamba anali nalo koma anabwereketsa mwana wina wasukulu. Wofalitsayu anauza mphunzitsiyo kuti atha kupanga dawunilodi bukuli pa jw.org.

Banja lina mumzinda wa Quevedo, linayamba kufufuza mayina a anthu omwe si a Mboni mufoni mwawo ndipo ankawalembera meseji yonena kuti: “Ndine wa Mboni za Yehova. Popeza kuti kwabwera mliri womwe ukukhudza dziko lonse, sitikumalalikira kunyumba ndi nyumba. Koma tingasangalale kwambiri kulankhula nanu kudzera pa vidiyokomfelensi.”

Ambiri mwa anthuwa anavomera. Mwachitsanzo, mayi wina amene poyamba sankafuna n’komwe kuti a Mboni amulalikire, anathokoza banjali chifukwa cholimbikitsa anthu pogwiritsa ntchito njira imeneyi. Mayiyu ananena kuti anali ndi nkhawa chifukwa cha mmene zinthu zilili panopa. Ndiyeno banjali linatumizira mayiyo PDF ya Galamukani! ya Na. 1 2020 yakuti “Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa.” Ulendo wotsatira atalumikizananso, mayiyo anayamikira kwambiri chifukwa cha magaziniyo ndipo anafotokoza kuti waiwerenga mobwerezabwereza.

Mtsikana wina yemwe ali ndi vuto losamva dzina lake Johana, wa m’chigawo cha Santo Domingo de los Tsáchilas, “analemba” kalata pogwiritsa ntchito zithunzi. * Kenako anajambula zithunzizo ndi foni yake n’kutumizira anthu onse omwe ali ndi vuto losamva, amene ali ndi manambala awo. Koma mmodzi wa anthu omwe analandira uthengawo anali mayi yemwe alibe vuto losamva. Nthawi yomweyo mayiyo anayankha kalatayo pomufunsa mafunso. Popeza kuti Johana sankamvetsa bwinobwino mafunsowo, mpainiya wina dzina lake Rhonda anamuthandiza ndipo anayankha mafunso a mayi wachidwiyo.

Mayiyo anauza Rhoda kuti zithunzi zomwe Johana anamutumizira zinamuchititsa chidwi kwambiri. Kenako anapempha mpainiyayo kuti amufotokozere ngati pali mavesi enanso a m’Baibulo ofotokoza zokhudza zomwe zikuchitika padzikoli. Rhonda anamuwerengera Luka 21:10, 11 n’kumutumizira malinki omuthandiza kupeza vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? ndi yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi? Mayiyu ndi wokonzeka kudzalankhulananso ndi mpainiyayu pa ulendo wotsatira.

Mofanana ndi Paulo yemwe anapitirizabe ‘kuchitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu’ ali m’ndende, nawonso abale athu akupitirizabe kulalikira pogwiritsa ntchito njira iliyonse yomwe yapezeka, ngakhale kuti akumachita zimenezi ali kunyumba zawo.—Machitidwe 28:23.

^ Popeza kuti anthu ambiri omwe ali ndi vuto losamva amavutika kumvetsa mawu omwe alembedwa, ofalitsa ambiri amajambula zithunzi zoyerekezera kuti afotokoze mfundo inayake kwa anthu a m’gawo la chinenero chamanja.