Pitani ku nkhani yake

AUGUST 20, 2019
PARAGUAY

A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Chiguarani

A Mboni za Yehova Atulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Chiguarani

Pa 16 August, 2019, a Mboni za Yehova anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chiguarani pamsonkhano wachigawo womwe unachitikira muholo ya pa Beteli yomwe ili mumzinda wa Capiatá ku Paraguay. M’bale Daniel González, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya Paraguay, anatulutsa Baibuloli pa tsiku loyamba la msonkhanowu. Panalinso malo ena okwana 13 omwe analumikizidwa ndipo ankaonera msonkhanowu pamasikirini. Anthu onse omwe anasonkhana pamene Baibuloli linkatulutsidwa anali 5,631.

Ngakhale kuti Chisipanishi ndi chimene anthu ambiri amayankhula m’dziko lonse la Paraguay, pafupifupi 90 peresenti ya anthu m’dzikoli amayankhulanso Chiguarani, chomwe ndi chinenero chawo chobadwira. Chifukwa cha zimenezi, pa mayiko onse a ku Latin America, ndi dziko la Paraguay lokha lomwe lili ndi anthu ambiri oyankhula chinenero chobadwira chofanana.

Mmodzi mwa anthu omwe anagwira nawo ntchito yomasulira Baibuloli, ananena kuti ngakhale pa nthawi imene Baibuloli linali lisanatulutsidwe, abale ndi alongo ambiri ankapemphera kwa Yehova m’chinenero chawo chobadwira cha Chiguarani. Iye anafotokoza kuti: “Tsopano Yehova azitiyankhula m’Chiguarani. Tayamba kale kumva kuti Yehova amatikonda ndi kutilemekeza. Panopa ndikumva kuti Yehova ndi Atate wanga kuposa mmene ndikamvera m’mbuyomu.”

Sitikukayikira kuti Baibulo la Chiguarani lithandiza ofalitsa 4,934 oyankhula Chiguarani ku Paraguay kuti azikonda komanso kuyamikira kwambiri Yehova ndiponso gulu lake. Tikukhulupirira kuti Baibuloli lithandiza anthu omwe aliwerenge kupindula ndi maganizo ofunika kwambiri a Mulungu.—Salimo 139:17.