Pitani ku nkhani yake

Abale ndi alongo a ku Poland amathandiza Akhristu anzawo a ku Ukraine, pokawayembekezera paboda kuti awalandire kapena powatumizira chithandizo

7 APRIL, 2022
POLAND

Abale ndi Alongo Akupereka Zinthu Zawo Mowolowa Manja pa Nthawi Yamavuto

Abale ndi Alongo Akusonyeza Mtima ‘Wochereza’

Abale ndi Alongo Akupereka Zinthu Zawo Mowolowa Manja pa Nthawi Yamavuto

Barbara Osmyk-Urban ndi ana ake, Jakub ndi Nina

Mlongo Barbara Osmyk-Urban amakhala ku Rzeszów m’dziko la Poland ndipo ali ndi ana omwe amalera yekha. Pa Kulambira kwa Pabanja, mlongoyu amaphunzitsa ana ake awiri, Jakub wazaka 10 ndi Nina wazaka 8, mmene angakhalire ochereza komanso kuchitira anthu ena chifundo. Banjali likuyesetsa kugwiritsa ntchito zomwe likuphunzira. Kuchokera pomwe nkhondo inayamba ku Ukraine pa 24 February 2022, banjali lakhala likusunga abale ndi alongo oposa 20 m’nyumba mwawo.

Pomwe abale ndi alongo akuthawa nkhondo m’dziko la Ukraine, Amboni a ku Poland komanso a m’mayiko ena akulandira Akhristu anzawowa m’nyumba zawo komanso akudzipereka kuwathandiza m’njira zambiri. Pofika pano, Amboni pafupifupi 11,000 a ku Ukraine anathawira ku Poland. Pa nthawi yankhondoyi, amuna a ku Ukraine oyambira zaka 18 mpaka 60 sakuloledwa kutuluka m’dzikolo. Komabe amuna okhawo omwe ali ndi ana aang’ono osachepera atatu, ndi omwe akuloledwa kutuluka.

Mlongo wina dzina lake Barbara ananena kuti: “Anthu omwe akuthawa nkhondo ku Ukraine ndi abale athu.” Ana a mlongoyu amakonda kwambiri abale ndi alongo omwe akuwasunga m’nyumba mwawo moti Jakub ndi Nina anasamuka m’zipinda zawo kuti abale ndi alongo afikiremo. Chifukwa chosiyana zilankhulo, amangomwetulirana, kuhagana komanso kulira limodzi. Patapita nthawi abale ndi alongowa atasamuka, Jakub ankawona kuti banja lawo latsala lokhalokha moti anapempha mayi ake kuti aitanenso abale ndi alongo ena.

Łukasz Cholewiński ndi Rafał Jankowski

M’bale Łukasz Cholewiński ndi M’bale Rafał Jankowski amadzipereka kukasiya chithandizo ku Ukraine. Abalewa anafotokoza kuti pamaulendowa, amaona akazi ndi ana ambirimbiri ataima paboda kwinaku akulira poyembekera kuti atuluke ndi kupita kumadera otetezeka. Koma M’bale Łukasz ananenanso kuti: “Chodabwitsa n’choti tikakumana ndi abale ndi alongo, amaoneka osangalala.”

Ulendo wopita ndi kubwerera ku Ukraine, umatenga maola 4. Chithandizo chikangofika, abale a ku Ukraine amakagawa chithandizocho m’madera onse a dzikolo. Abale ndi alongo ambiri amadzipereka kukasiya chithandizo ku Ukraine ngakhale kuti kuchita zimenezi ndi koopsa. M’bale Rafał ananena kuti: “Timaona kuti ndi mwayi waukulu kugwira nawo ntchitoyi.”

Mlongo wina wa ku Rzeszów, dzina lake Elżbieta Ustrzycka, anafotokoza mmene anamvera atasunga abale ndi alongo omwe anathawa ku Ukraine. Iye anati: “Zinandikhudza kwambiri akulu atabwera kunyumba kwathu pakati pausiku ali ndi mabanja a ku Ukraine, ana awo ali m’manja akugona. Zimenezi zidzanditengera nthawi yaitali kuti ndiiwale.”

Bartłomiej ndi Estera Figura

M’bale Bartłomiej Figura, ndi mmodzi wa akulu omwe akugwira ntchito mosatopa. Iye ndi mkazi wake Estera, amapita kuboda kapena kumasiteshoni a sitima kukatenga Akhristu anzawo n’kupita nawo kumadera otetezeka. Nthawi zina banjali limalolera kukakhala kwina ndi cholinga choti m’nyumba mwawo mufikire alendowa. Nthawi zinanso ngati angakwanitse, amatha kupereka zinthu zina zofunika kwa abalewa.

M’bale Figura ananena kuti: “Timakondana kwambiri ndi abale ndi alongo athuwa. Tikamadzipereka kugwira nawo ntchitoyi, timaona mmene Yehova amapatsira abale ndi alongo zinthu zenizeni zomwe akufunikira.”

Panopo, abale a ku Poland apakira makatoni achithandizo okwana pafupifupi 23,000 kuphatikizapo chakudya, zipangizo zodzitetezera ku matenda komanso zinthu zina.

Ana a ku Poland limodzi ndi makolo awo akugwiritsa ntchito ma apu a JW Language ndi JW Library polemba makadi mu Chiyukireniya. Akamaliza amaika makadiwo m’makatoni achithandizo

Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova apitiriza kuthandiza abale ndi alongo athu a ku Ukraine powapatsa zinthu zofunikira pomwe Akhristu anzawo akupitiriza kuwathandiza mowolowa manja.—Miyambo 11:24; Aroma 12:13.