Pitani ku nkhani yake

Andrey ndi mkazi wake Svetlana ali panja pa khoti pambuyo pa chigamulo choti m’baleyu amasulidwe pa ukaidi wosachoka panyumba

AUGUST 22, 2019
RUSSIA

Khoti la Apilo Lalamula Kuti M’bale Andrey Suvorkov Amasulidwe pa Ukaidi Wosachoka Panyumba

Khoti la Apilo Lalamula Kuti M’bale Andrey Suvorkov Amasulidwe pa Ukaidi Wosachoka Panyumba

Pa 13 August, 2019, khoti la apilo la mumzinda wa Kirov linalamula kuti M’bale Andrey Suvorkov wazaka 26, amasulidwe pa ukaidi wosachoka panyumba. Ngakhale kuti M’bale Suvorkov panopa wapatsidwa ufulu wambiri, mlandu wake udakalipobe.

Monga mmene nkhani ina inanenera m’mbuyomu, M’bale Suvorkov anamangidwa limodzi ndi bambo ake omupeza komanso abale ena atatu pa 9 October, 2018, pamene apolisi a mumzinda wa Kirov ndiponso apolisi apadera ovala zobisa nkhope anathyola n’kulowa m’nyumba 19 za mumzindawu.

Pofotokoza zimene zinachitika pamene apolisi anachita chipikisheni m’nyumba yake, M’bale Suvorkov anati: “Zinthu zathu zambiri zofunika zinatengedwa. Koma ine ndi mkazi wanga sitinadandaule nazo chifukwa nthawi zonse tinkayesetsa kukhala moyo wosalira zambiri ndipo sitinkaganizira kwambiri za katundu. Malangizo opezeka pa Mateyu 6:21 akuti, ‘pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko,’ anatithandiza kuti tisatekeseke.”

Pambuyo pa chipikishenicho, M’bale Suvorkov, bambo ake omupeza, komanso abale atatu aja anawatsegulira milandu chifukwa choimba nyimbo za Ufumu, kuphunzira mabuku a chipembedzo chake, komanso kupezeka ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chirasha. Onse anawatsekera m’ndende yongoyembekezera pamene ankadikira kuti khoti ligamule kuti atulutsidwe kapena atumizidwe kundende poyembekezera kuwazenga mlandu.

M’bale Suvorkov akufotokoza zomwe zinachitika: “Ndinakhala m’ndende yongoyembekezera kwa masiku awiri. Nditangofika m’ndendeyi, sindinasiye kupemphera. Sindinkakayikira kuti Yehova ankandimvetsera ndiponso kuti andithandiza. Ndinakumbukira nyimbo za Ufumu ndipo ndinaziimba. Kenako ndinakumbukira nyimbo zoposa 50 ndi mawu ake omwe.”

Khoti linagamula kuti M’bale Suvorkov komanso abale enawo aikidwe m’ndende poyembekezera kuwazenga mlandu. Mlungu woyamba kukhala m’ndende, M’bale Suvorkov ankaganizira zothandiza anthu ena. Iye akukumbukira kuti: “Ndinaganiza zoti ndizitchula mayina a abale m’mapemphero anga komanso kulembera makalata anthu omwe ndinkakumbukira maadiresi awo. Zimenezi zinandipangitsa kuti ndizisangalala.”—Machitidwe 20:35.

Pamene miyezi inkadutsa, abale ena onse anauzidwa kuti akakhale paukaidi wosachoka panyumba, kupatulapo M’bale Andrzej Oniszczuk. M’bale Suvorkov ndi m’bale woyamba wa ku Kirov kumasulidwa pa ukaidi wosachoka panyumba.

M’bale Suvorkov anati: “Ndikaganizira zomwe zinachitika, ndimasangalala kwambiri kuti ndinakhalapo kundende. . . . Sindikudziwa kuti m’tsogolomu muchitika zotani kapena ngati ndidzaikidwenso m’ndende. Ndikukhulupirira kuti Yehova komanso gulu lake adzandithandiza, ngakhale nditakhala m’ndende. Panopa sindikuopa kuikidwa m’ndende.”