Pitani ku nkhani yake

APRIL 1, 2019
RUSSIA

Wa Mboni za Yehova Winanso Amupeza Wolakwa ku Russia

Wa Mboni za Yehova Winanso Amupeza Wolakwa ku Russia

Pa 1 April, 2019, khoti la ku Russia lomwe linagamula kuti M’bale Dennis Christensen akhale m’ndende zaka 6, linapezanso a Sergey Skrynnikov a zaka 56 kuti ndi wolakwa chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira monga wa Mboni za Yehova. Khotilo linanena kuti a Skrynnikov alipire chindapusa cha ndalama zambiri zokwana madola 5,348. A Skrynnikov sanagamulidwe kuti akakhale m’ndende, ngakhale kuti maloya a mbali yomwe inakawasumira mlandu amafuna kuti akhale m’ndende zaka zitatu.

M’bale Skrynnikov ndi mkazi wake Nina, ali ndi mwana mmodzi wamkazi. Iwo amathandiza banja la mwana wawoyu limodzi zidzukulu zawo 5. Kuwonjezera pamenepo, banja la a Skrynnikov lilinso ndi udindo wosamalira makolo a Nina omwe ndi okalamba.

Pamene mlandu wake unkazengedwa m’khoti, M’bale Skrynnikov anafotokoza mwaulemu komanso momveka bwino zokhudza zimene amakhulupirira. Mwa zina, m’baleyu anati: “Munthu yemwe alibe chikhulupiriro mwa Mulungu atakumana ndi zimene ndakumana nazo inezi, akhoza kutaya mtima. . . . Koma monga wa Mboni za Yehova, sindikutaya mtima chifukwa ndili ndi chikhulupiriro. Ngati Mulungu angalole kuti ndikakhale m’ndende kwa zaka zitatu, sindikuyenera kuona zaka zimenezi ngati chilango, koma ngati mwayi wapadera woti ndikatumikire kumalo atsopano. Ndiye sindikudandaula. . . . Mulungu ndi mmodzi ndipo akhoza kutithandiza kaya tili m’ndende kapena ayi. Choncho, sikuti iye amatitaya. Iye amakhala nafe kulikonse komwe tingakhale bola ngati tili okhulupirika kwa iye.”

Zimatilimbikitsa tikaona chikhulupiriro cholimba chomwe abale athu, monga M’bale Skrynnikov, ali nacho. Tikaganizira mayesero aakulu omwe akukumana nawo, zimatikumbutsa mawu omwe Paulo ananena m’pemphero akuti: “Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirika kwanu, kuti mukhale ndi chiyembekezo chachikulu mwa mphamvu ya mzimu woyera.”—Aroma 15:13.