Pitani ku nkhani yake

Nyumba yomwe Khoti Lalikulu Kwambiri ku Sweden linkamvetsera mlandu

DECEMBER 18, 2019
SWEDEN

Khoti la ku Sweden Lagamula Mokomera a Mboni za Yehova

Khoti la ku Sweden Lagamula Mokomera a Mboni za Yehova

Kungoyambira pa 1 January, 2000, boma la Sweden lakhala likupereka ndalama zothandizira mabungwe a zipembedzo potsatira zimene zili mu lamulo la m’dzikoli loti zipembedzo zizipatsidwa thandizo la ndalama. Komabe, boma limapereka thandizoli kugulu la chipembedzo lokhalo lomwe “limalimbikitsa mfundo za makhalidwe abwino zothandiza kuti anthu azichitira zinthu limodzi mogwirizana” komanso “lomwe limatenga nawo mbali pothandiza anthu m’dera lawo.”

Ngakhale kuti boma la Sweden linavomereza kuti zipembedzo zambiri zipatsidwe thandizo la ndalama, kuyambira mu 2007 lakhala likukana mobwerezabwereza kupereka thandizoli kwa a Mboni za Yehova. Bomali silinagwirizane ndi zimene timakhulupirira pa nkhani yochita nawo zandale.

Abale athuwa analibe njira ina kupatulapo kukadandaula za nkhaniyi kukhoti n’cholinga choti boma la Sweden liwaganizire ndipo anachita zimenezi kwa maulendo atatu chifukwa zimene bomali linachita ndi kukondera. Pa ulendo uliwonse, Khoti Lalikulu Kwambiri m’dzikolo linagamula kuti zimene boma linachita pokaniza kuthandiza a Mboni n’zosemphana ndi malamulo ndipo likufunika kusintha.

Kenako pa 24 October, 2019, boma la Sweden linasintha maganizo ake ndipo linanena kuti a Mboni za Yehova “amatsatira zonse zofunikira mogwirizana ndi malamulo” ndipo ndi oyenerera kupatsidwa thandizo la boma.

Posachedwapa, nkhani ngati yomweyi yachitikanso ku Norway. M’dzikolo, boma lakhala likupereka thandizo la ndalama ku zipembedzo zonse kuphatikizapo Mboni za Yehova. Koma m’miyezi yaposachedwapa, boma linapemphedwa kuti liunikenso ngati zili zoyenera kuti lizipereka thandizo kwa a Mboni za Yehova chifukwa choti sachita nawo zandale. Abale athu atafunsidwa za nkhaniyi, anafotokoza mfundo zolondola zokhudza zimene timakhulupirira pa nkhani zandale. Abalewa anaperekanso umboni wa zimene Khoti Lalikulu Kwambiri m’dziko la Sweden linagamula motikomera komanso zigamulo zinanso zotikomera za makhoti ndiponso maboma a Germany ndi Italy.

Ndife osangalala kuti pa 18 November, 2019, akuluakulu a boma la Norway anagamula kuti boma silisiya kupereka ndalama zothandiza Mboni za Yehova ndipo anamaliza n’kunena kuti: “Kuvota pa nthawi ya zisankho ndi ufulu wa nzika iliyonse ya dziko la Norway koma sikuti ndi lamulo. Zikuoneka kuti a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti asamagwiritse ntchito ufulu wovota. Boma likuvomereza kuti malamulo akupereka ufulu pa nkhaniyi ndipo boma liyenera kumapereka ndalama zothandiza Mboni za Yehova.”

M’bale Dag-Erik Kristoffersen wa ku ofesi ya nthambi ya Scandinavia anati: “Tikusangalala kuti boma layamba kuona kuti timachita zinthu zothandiza anthu m’dera lathu. Tikukhulupirira kuti maboma enanso omwe amapereka thandizo ku zipembedzo aphunzirapo pa chigamulo chimenechi.” Koposa zonse, tikuthokoza kwambiri Yehova yemwe ndi Wotipatsa Malamulo wamkulu.—Yesaya 33:22.