Pitani ku nkhani yake

Kodi Mapeto a Dzikoli Adzafika Liti?

Kodi Mapeto a Dzikoli Adzafika Liti?

Yankho la m’Baibulo

 Kuti tidziwe nthawi imene dzikoli lidzathe, tiyenera kudziwanso zimene Baibulo limatanthauza likamanena za “dziko.” Mawu achigiriki akuti koʹsmos, nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “dziko” ndipo nthawi zambiri amatanthauza anthu, makamaka anthu amene sakuchita zimene Mulungu amafuna. (Yohane 15:18, 19; 2 Petulo 2:5) Mawu akuti koʹsmos, nthawi zinanso amatanthauza zinthu zonse zam’dzikoli zimene anthu amazigwiritsa ntchito.​—1 Akorinto 7:31; 1 Yohane 2:15, 16. a

Kodi mawu oti “mapeto a dzikoli” amatanthauza chiyani?

 Mawu akuti “mapeto a dzikoli,” omwe amapezeka m’Mabaibulo ambiri angamasuliridwenso kuti “mapeto a nthawi ino.” (Mateyu 24:3) Mawuwa sakutanthauza kuwonongedwa kwa dziko lapansi kapena anthu onse apadzikoli. Koma akutanthauza kuti zinthu zimene anthu amachita m’dzikoli masiku ano zidzatha.​—1 Yohane 2:17.

 Baibulo limaphunzitsa kuti “ochita zoipa adzaphedwa” n’cholinga choti anthu abwino azidzakhala mosangalala padzikoli. (Salimo 37:9-11) Anthu oipa adzawonongedwa pa nthawi ya “chisautso chachikulu,” chomwe chidzafike pachimake pa nkhondo ya Aramagedo.​—Mateyu 24:21, 22; Chivumbulutso 16:14, 16.

Kodi mapeto a dzikoli adzafika liti?

 Yesu ananena kuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36, 42) Iye ananenanso kuti mapeto adzafika modzidzimutsa “pa ola limene simukuliganizira.”​—Mateyu 24:44.

 Ngakhale kuti sitikudziwa tsiku kapena ola lake, Yesu anapereka “chizindikiro,” kapena kuti zochitika zosiyanasiyana, zimene zikanathandiza anthu kuzindikira nthawi yoti mapeto atsala pang’ono kufika. (Mateyu 24:3, 7-14) Baibulo limanena kuti nthawiyi ndi “nthawi yamapeto” kapena kuti “masiku otsiriza.”​—Danieli 12:4; 2 Timoteyo 3:1-5.

Kodi dzikoli likadzatha ndiye kuti chilichonse chidzawonongedwa?

 Ayi, dziko lenilenili silidzatha chifukwa Baibulo limanena kuti dziko “silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.” (Salimo 104:5) Ndipotu padzikoli pazidzakhala anthu ambiri. Tikutero chifukwa Baibulo limalonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Mulungu adzakwaniritsa zimene ankafuna pamene ankalenga anthu. Padzikoli padzakhala:

a M’Mabaibulo ena, mawu achigiriki akuti ai·onʹ anamasuliridwanso kuti “dziko.” Mawuwa akamasuliridwa kuti “dziko,” amatanthauza zofanana ndi zimene mawu akuti koʹsmos amatanthauza nthawi zina. Tikutero chifukwa chakuti amanena za zinthu zonse zam’dzikoli zimene anthu amazigwiritsa ntchito.