Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Chivumbulutso 21:1—“Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano”

Chivumbulutso 21:1—“Kumwamba Kwatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano”

 “Tsopano ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, pakuti kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka, ndipo kulibenso nyanja.”—Chivumbulutso 21:1, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Ndipo ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.”—Chivumbulutso 21:1, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Chivumbulutso 21:1

 Vesili limafotokoza zinthu mophiphiritsa pofuna kusonyeza kuti Ufumu wakumwamba wa Mulungu udzalowa m’malo mwa maboma onse a anthu. Ufumuwo udzachotsa anthu oipa ndipo udzalamulira anthu omwe ndi ofunitsitsa kumvera ulamulirowo.

 Buku la Chivumbulutso limafotokoza zinthu pogwiritsa ntchito “zizindikiro.” (Chivumbulutso 1:1) Choncho m’pomveka kunena kuti kumwamba ndi dziko lapansi zomwe zatchulidwa m’vesili zangokhala zizindikiro chabe, osati kumwamba kwenikweni kapenanso dziko lapansi lenileni. Kuwonjezera pamenepa, mawu ophiphiritsa akuti “kumwamba kwatsopano” ndi “dziko lapansi latsopano,” anatchulidwanso m’mavesi ena a m’Baibulo. (Yesaya 65:17; 66:22; 2 Petulo 3:13) Kufufuza mosamala mavesi amenewa komanso nkhani zotchulidwa m’mavesi ena, kumatithandiza kumvetsa tanthauzo lake.

 “Kumwamba kwatsopano.” Nthawi zina, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “kumwamba,” ponena za maulamuliro kapena maboma. (Yesaya 14:12-14; Danieli 4:25, 26) Buku lina lofotokoza mavesi a m’Baibulo linanena kuti m’maulosi, “kumwamba kumaimira mphamvu za ulamuliro zomwe maboma amakhala nazo.” a Choncho n’zoonekeratu kuti mawu a pa Chivumbulutso 21:1, akuti “kumwamba kwatsopano” akuimira Ufumu wa Mulungu. Boma lakumwambali lomwe nthawi zina limatchedwa kuti “Ufumu wakumwamba” limatchulidwa mobwerezabwereza m’buku la Chivumbulutso ndi m’mabuku ena a m’Baibulo. (Mateyu 4:17; Machitidwe 19:8; 2 Timoteyo 4:18; Chivumbulutso 1:9; 5:10; 11:15; 12:10) Ufumu wa Mulungu womwe Mfumu yake ndi Yesu, udzalowa m’malo mwa “kumwamba kwakale” komwe kukuimira maboma onse opangidwa ndi anthu ochimwa.—Danieli 2:44; Luka 1:31-33; Chivumbulutso 19:11-18.

 “Dziko lapansi latsopano.” Baibulo limanena kuti dziko lapansi lenilenili, silidzawonongeka kapena kulowedwa m’malo. (Salimo 104:5; Mlaliki 1:4) Ndiye kodi dziko lapansi lophiphiritsa likuimira chiyani? Nthawi zambiri, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “dziko lapansi,” ponena za anthu. (Genesis 11:1; 1 Mbiri 16:31; Salimo 66:4; 96:1) Choncho mawu akuti “dziko lapansi latsopano,” ayenera kutanthauza anthu omwe ndi ofunitsitsa kumvera boma lakumwamba la Mulungu. “Dziko lapansi lakale” kapena kuti anthu omwe samvera Ufumu wa Mulungu, sadzakhalaponso.

 “Kulibenso nyanja.” Mogwirizana ndi mbali yomaliza ya Chivumbulutso 21:1, mawu akuti “nyanja” nawonso ndi ophiphiritsa. Nthawi zambiri panyanja pamakhala chimphepo ndipo nyanjayo siichedwa kuwinduka. Choncho nyanja ikuimira anthu okwiya omwenso ndi otalikirana ndi Mulungu. (Yesaya 17:12, 13; 57:20; Chivumbulutso 17:1, 15) Anthu amenewa nawonso sadzakhalapo. Ndipo Salimo 37:10 limati: “Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.”

Mawu onse a pa Chivumbulutso 21:1

 Buku la Chivumbulutso linaneneratu zomwe zidzachitike “m’tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:10) Mogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo, tsikuli linayamba mu 1914 pamene Yesu anayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. b Koma iye atakhala Mfumu, sanayambe kulamulira dziko lonse lapansi nthawi yomweyo. Ndipotu maulosi ena amasonyeza kuti makhalidwe a anthu adzaipa kwambiri kumayambiriro kwa ‘tsiku la Ambuye.’ Nthawi imeneyi imatchedwa kuti “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5, 13; Mateyu 24:3, 7; Chivumbulutso 6:1-8; 12:12) Nthawi yapadera komanso yodzadza ndi mavutoyi ikadzatha, Ufumu wa Mulungu udzachotsa kumwamba kwakale kophiphiritsa ndi dziko lapansi lakale lophiphiritsa, kenako n’kubweretsa bata ndi mtendere. Pambuyo pake, “dziko lapansi latsopano,” kapena kuti nzika za Ufumuwo, zidzasangalala kukhala m’dziko la mtendere komanso zidzakhala ndi moyo wathanzi.—Chivumbulutso 21:3, 4.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti muone mfundo zokhudza buku la Chivumbulutso.

a McClintock and Strong’s Cyclopedia (1891), Volume IV, tsamba 122.