Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

WATCHTOWER LIBRARY

Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri​—Watchtower Library

Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri​—Watchtower Library

Kuti muthe kugwiritsa ntchito Watchtower Library, kompyuta kapena laputopu yanu ikhale yogwirizana ndi processor ya Pentium kapena ina yamphamvu kuposa imeneyi. Ikhale yoti muli Microsoft Windows 7 kapena kuposa ndipo RAM yake ikhale yosachepera 48 MB komanso hard drive ya kompyutayo ikhale yoyambira 3 GB ku C: drive.

Dziwani izi: Ngati kompyuta yanu ili ndi Microsoft Windows 7, choyamba muyenera kupanga kaye dawunilodi ndi kuikamo pulogalamu ya pakompyuta yothandiza kuti kompyutayo ikwanitse kutsegula failo ya ISO. Mungathe kupeza pulogalamuyi pa webusaiti ya Microsoft.

 

Ngati mukulandira mobwerezabwereza meseji yakuti Watchtower Library yalephera kuika zinthu zatsopano, mutsatire njira zotsatirazi poika nokha:

  1. Pitani patsamba lakuti Pangani Update Watchtower Library pa jw.org.

  2. Pangani dawunilodi Failo ya Watchtower Library Yoikira Zinthu Zatsopano m’chilankhulo chanu..

  3. Tsatirani malangizo pa mutu wakuti “Gwiritsani Ntchito Failo Yoikira Zinthu Zatsopano.”

Ngati sizikuthekabe, tsatirani njira izi:

  1. Mu File Explorer, tsegulani pa “C:\ProgramData\Watchtower\WTLibrary.”

  2. Dilitani mafailo awiriwa:

    • a. ca-bundle.zip

    • b. cert.pem

Ngati mukuvutika kutsatira njira zili pamwambazi, pemphani mnzanu amene amadziwa bwino Watchtower Library kuti akuthandizeni, kapena funsani ku ofesi ya nthambi imene ili pafupi.

 

Mnzanu amene amadziwa bwino Watchtower Library akhoza kukuthandizani. Ngati sizingatheke, funsani ku ofesi ya nthambi yathu imene ili pafupi.