Bwelelani kwa Yehova

Yehova akufunafuna nkhosa zake zosocela, ndipo akupempha kuti mubwelele kwa iye.

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kalatayi ndi pempho locokela ku Bungwe Lolamulila kuti atumiki a Mulungu amene anacoka m’khola abwelele.

MBALI 1

“Nkhosa Zosocela Ndidzazifunafuna”

Kodi Yehova amaona nkhosa yosocela ngati munthu woipa amene sangabwelele kwa iye?

MBALI 2

Nkhawa​—“Timapanikizidwa Mwamtundu Uliwonse”

Ngati mukuvutika mtima cifukwa cakuti simukwanitsa kutumikila Yehova monga kale, pali cimene mungacite kuti Mulungu akuthandizeni ndi mphamvu zake.

MBALI 3

Kukhumudwa​—Tikakhala Ndi “Cifukwa Codandaulila”

Mfundo zitatu za m’Baibulo zingakuthandizeni kupilila ngati Mkristu mnzanu wakulakwilani.

MBALI 4

Kudziimba Mlandu​—“Ndiyeletseni ku Chimo Langa”

N’ciani cimene muyenela kucita kuti mukhale ndi cikumbumtima coyela?

MBALI 5

Bwelelani kwa “Mbusa Wanu ndi Woyang’anila Miyoyo Yanu”

Ndikafuna kubwelela kwa Yehova, kodi ndingayambile pati? Nanga abale ndi alongo mumpingo adzandiona bwanji?

Kumapeto

Kodi nthawi zina mumakumbukila mmene munali kusangalalila ndi anthu a Yehova?