Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 5

Bwelelani kwa “Mbusa Wanu ndi Woyang’anila Miyoyo Yanu”

Bwelelani kwa “Mbusa Wanu ndi Woyang’anila Miyoyo Yanu”

Mwina poŵelenga kabuku kano, mwapeza kuti kakukamba zimene zinakucitikilani. Ngati ndi conco, dziŵani kuti simuli nokha. Pali atumiki a Mulungu ambili okhulupilika, amakono ndiponso ochulidwa m’Baibulo, amene akumana ndi zopinga ngati zimenezi. Yehova anawathandiza kugonjetsa zopingazo, ndipo inunso adzakuthandizani.

Yehova adzakulandilani mukabwelela kwa iye

DZIŴANI kuti Yehova adzakulandilani mukabwelela kwa iye. Adzakuthandizaninso kulimbana ndi nkhawa, kusiya kudziimba mlandu, ndi kukhala ndi cikumbumtima coyela. Cikumbumtima coyela cidzakupatsani mtendele mumtima ndi m’maganizo. Ndiyeno mwina mudzafuna kuyambanso kutumikila Yehova pamodzi ndi alambili anzanu. Mukacita zimenezi, mudzafanana ndi Akristu ena oyambilila, amene mtumwi Petulo anawalembela kuti: “Munali ngati nkhosa zosocela, koma tsopano mwabwelela kwa mbusa wanu ndi woyang’anila miyoyo yanu.”—1 Petulo 2:25.

Kunena zoona, palibe cinthu cina cabwino kwambili cimene mungacite kuposa kubwelela kwa Yehova. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti mukabwelela kwa Yehova, mudzakondweletsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Inu mukudziŵa kuti zocita zathu zimam’khudza Yehova. Ndipo Yehova satikakamiza kuti tizim’konda ndi kum’tumikila. (Deuteronomo 30:19, 20) Katswili wina wa Baibulo anati: “Palibe amene angakutsegulileni mtima wanu. Muyenela kuutsegula nokha.” Tingatsegule mtima wathu ngati tilambila Yehova cifukwa com’konda ndi mtima wathu wonse. Tikatelo, timapatsa Mulungu mphatso yamtengo wapatali. Mphatso imeneyo ndi kukhulupilika kwathu, ndipo mtima wake umakondwela kwambili. Inde, kulambila Yehova m’njila yoyenela kumatibweletsela cimwemwe cosaneneka.—Machitidwe 20:35; Chivumbulutso 4:11.

Mukayamba kulambila Mulungu, mudzakhutilitsanso zosoŵa zanu za kuuzimu. (Mateyu 5:3) Tikunena conco cifukwa cakuti padziko lonse lapansi, anthu sadziŵa cifukwa cake tili ndi moyo. Iwo ali ndi njala yofuna kudziŵa colinga ca moyo. Ali ndi njala imeneyi cifukwa ndi mmene Yehova anawalengela. Iye anatilenga mwa njila yakuti tizikhala okhutila pom’tumikila. Conco, ngati tilambila Yehova cifukwa com’konda, timakhala okhutila kwambili.—Salimo 63:1-5.

Dziŵani kuti Yehova akufuna kuti mubwelele kwa iye. Kodi mungatsimikize bwanji zimenezi? Taganizilani mfundo izi: Mapemphelo ambili anapelekedwa pokonza kabukuka. Mwina munamva za kabukuka kwa mkulu mumpingo kapena kwa wokhulupilila mnzanu. Ndiyeno, mutakalandila munayamba kuŵelenga ndi kutsatila malangizo ake. Zonsezi ndi umboni wakuti Yehova sanakuiŵaleni iyai. M’malo mwake, akukukokani pang’onopan’ono kuti mubwelele kwa iye.—Yohane 6:44.

N’zotonthoza kwambili kudziŵa kuti Yehova saiŵala atumiki ake osocela. Mlongo wina, dzina lake Donna, anafika pomvetsetsa mfundo imeneyi. Iye anati: “Ndinasiya coonadi pang’onopang’ono. Koma sindinaleke kuganizila mau a pa Salimo 139:23, 24 omwe amati: ‘Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziŵa mtima wanga. Ndisanthuleni ndi kudziŵa malingalilo anga amene akundisoŵetsa mtendele, ndipo muone ngati mwa ine muli ciliconse cimene cikundicititsa kuyenda m’njila yoipa, ndipo munditsogolele m’njila yamuyaya.’ Ndinali kudziŵa kuti kudzikoku si kwathu iyai. Kwathu ndi m’gulu la Yehova. Ndipo ndinayamba kuzindikila kuti Yehova sananditaye, ndingofunika kubwelela kwa iye. Pano ndine wokondwa kwambili kuti ndinacita zimenezo.”

“Ndinayamba kuzindikila kuti Yehova sananditaye, ndingofunika kubwelela kwa iye”

Ife tikukupemphelelani ndi mtima wonse kuti inunso mupeze “cimwemwe cimene Yehova amapeleka.” (Nehemiya 8:10) Ndipo mukabwelela kwa Yehova, zinthu zidzakuyendelani bwino kwambili.

[DO NOT SET] This page will not contain any WEB tags or SEO information.