Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NSANJA YA MLONDA Na. 3 2018 | Kodi Mulungu Amakudelani Nkhawa?

KODI MULUNGU AMAKUDELANI NKHAWA?

Masoka aakulu akacitika kapena pamene anthu avutika na kufa, tingadzifunse ngati Mulungu amaona komanso kukhudzidwa na zimenezi. Baibo imakamba kuti:

“Pakuti maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzelo lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyila anthu ocita zoipa.”1 Petulo 3:12.

Nsanja ya Mlonda ino, ionetsa mmene Mulungu amatithandizila komanso zimene akucita kuti acotsepo mavuto onse.

 

“Kodi Mulungu Anali Kuti?”

Kodi vuto lothetsa nzelu limene linakucitikilani limakupangitsani kukaikila ngati mulungu amakudelani nkhawa imwe pamwekha?

Kodi Mulungu Amakudelani Nkhawa?

Kodi pali umboni wabwanji woonetsa kuti Mulungu amakudelani nkhawa?

Kodi Mulungu Amakudziŵani Bwino?

Mulungu amatidziŵa mwapadela kwambili. Amadziŵa mmene tinapangidwila. Izi zimatitsimikizila kuti zoonadi amadziŵa zonse zokhudza ife.

Kodi Mulungu Ni Wacifundo Zoona?

Baibo imatitsimikizila kuti Mulungu amatidela nkhawa, kutimvetsetsa, na kutimvelela cifundo.

Mavuto—Kodi Ni Cilango Cocokela Kwa Mulungu?

Kodi Mulungu amaseŵenzetsa matenda kapena masoka a zacilengedwe pofuna kulanga anthu pa macimo awo?

Nanga N’ndani Amapangitsa Mavuto?

Baibo imafotokoza zinthu zitatu zimene zimapangitsa anthu kuvutika.

Posacedwa Mulungu Adzacotsapo Mavuto Onse

Kodi tingadziŵe bwanji kuti posacedwa Mulungu adzacitapo kanthu kuti acotsepo mavuto onse na kupanda cilungamo?

Mmene Mungapindulile na Cisamalilo ca Mulungu

Malemba amatithandiza kukhala na cikhulupililo m’malonjezo a Mulungu okhudza tsogolo labwino.

Kodi Mulungu Amamvela Bwanji Akaona Kuti Muvutika?

Mavesi awa a m’Baibo, angakuthandizeni kudziŵa mmene Mulungu amamvelela pa nkhani ya mavuto.