Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Kodi Mulungu Anali Kuti?”

“Kodi Mulungu Anali Kuti?”

“NTHAWI ZAMBILI NIMADZIFUNSA KUTI: KODI MULUNGU ANALI KUTI?” Anakamba conco Papa Benedict wa namba 16 pamene anayendela msasa wa cibalo wa Auschwitz, ku Poland.

PAKACITIKA MASOKA AAKULU, KODI MUMADZIFUNSA KUTI, ‘KODI MULUNGU ANALI KUTI?’ NANGA BWANJI MU UMOYO WANU, KODI MUNAKUMANAPO NA VUTO LOTHETSA NZELU, IMENE INAKUPANGITSANI KUKAIKILA NGATI MULUNGU AMAKUDELANI NKHAWA IMWE PAMWEKHA?

Mwina mumamvela mmene Sheila wa ku America anali kumvelela. Analeledwa m’banja lokonda kwambili za cipembedzo. Iye anati: “Kuyambila nili mwana n’nali kukhulupilila kuti Mulungu aliko cifukwa ndiye anatilenga. Koma sin’naganizilepo ngati amanikonda. N’nali kuganiza kuti amaniyang’ana, koma capatali. N’nali kudziŵa kuti Mulungu sanizonda, koma sin’nali kukhulupilila kuti amanidela nkhawa.” N’cifukwa ciani Sheila anali kukaikila? Iye anati: “Banja lathu linakumana na mavuto motsatizana-tsatizana, ndipo zinali kuoneka monga kuti Mulungu sanali kutithandiza olo pang’ono.”

Mofanana ndi Sheila, mwina mumakhulupilila kuti Mulungu Wamphamvuzonse alikodi. Koma mwina mumakaikila ngati amakudelani nkhawa. Munthu wolungama Yobu, anali kukhulupilila kuti Mlengi ali na mphamvu komanso nzelu, koma anali kukaikila ngati amam’dela nkhawa. (Yobu 2:3; 9:4) Pamene Yobu anakumana na mavuto motsatizana-tsatizana, komanso popanda ciyembekezo cakuti mavutowo adzasila, anafunsa Mulungu kuti: “N’cifukwa ciyani mukubisa nkhope yanu, n’kunditenga ine ngati mdani wanu?”—Yobu 13:24.

Kodi Baibo imakamba ciani? Kodi tiyenela kuimba mlandu Mulungu pakacitika masoka aakulu? Kodi paliko umboni woonetsa kuti Mulungu amadela nkhawa anthu onse, komanso aliyense payekha-payekha? Kodi n’zotheka munthu kudziŵa ngati Mulungu amatidela nkhawa, kutimvetsetsa, kuticitila cifundo, komanso kutithandiza tikakumana na mavuto?

Nkhani zotsatila, zidzafotokoza zimene cilengedwe cimatiphunzitsa pa nkhani yakuti Mulungu amatidela nkhawa. (Aroma 1:20) Ndiyeno, tidzaonanso bwino-bwino zimene Baibo imakamba zakuti Mulungu amatidela nkhawa. ‘Mukamudziwa’ bwino kupitila m’cilengedwe komanso m’Mau ake, m’pamenenso mudzakhala otsimikiza kuti “amakudelani nkhawa.”—1 Yohane 2:3; 1 Petulo 5:7.