Wolembedwa ndi Yohane 8:12-59

  • Atate anachitira umboni za Yesu (12-30)

    • Yesu ndi “kuwala kwa dziko” (12)

  • Ana a Abulahamu (31-41)

    • “Choonadi chidzakumasulani” (32)

  • Ana a Mdyerekezi (42-47)

  • Yesu ndi Abulahamu (48-59)

8   12  Kenako Yesu analankhula nawonso kuti: “Ine ndine kuwala kwa dziko.+ Aliyense wonditsatira ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala ndi kuwala+ kwa moyo.” 13  Choncho Afarisi anauza Yesu kuti: “Iwe umadzichitira wekha umboni koma umboni wakowo si woona ayi.” 14  Poyankha Yesu anati: “Ngakhale kuti ndimadzichitira ndekha umboni, umboni wanga ndi woona, chifukwa ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita.+ Koma inu simukudziwa kumene ndinachokera komanso kumene ndikupita. 15  Inu mumaweruza potengera mmene munthu akuonekera.*+ Inetu sindiweruza munthu aliyense. 16  Koma ndikati ndiweruze, chiweruzo changa chimakhala cholungama, chifukwa sindiweruza ndekha koma ine limodzi ndi Atate amene anandituma timaweruzira limodzi.+ 17  Ndiponso mʼChilamulo chanu chomwechi analembamo kuti: ‘Umboni wa anthu awiri ndi woona.’+ 18  Ineyo pandekha ndimadzichitira umboni ndipo Atate amene anandituma amandichitiranso umboni.”+ 19  Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Atate wako ali kuti?” Yesu anayankha kuti: “Inu simukundidziwa komanso simukudziwa Atate wanga.+ Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga.”+ 20  Yesu ananena mawu amenewa ali mʼmalo osungira zopereka+ pamene ankaphunzitsa mʼkachisi. Koma palibe amene anamugwira, chifukwa nthawi yake inali isanakwanebe.+ 21  Choncho iye anawauzanso kuti: “Ine ndikuchoka ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa mudakali ochimwa.+ Kumene ine ndikupita inu simungathe kupitako.”+ 22  Ndiye Ayudawo anayamba kunena kuti: “Kodi akufuna kudzipha? Nanga nʼchifukwa chiyani akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita inu simungathe kupitako?’” 23  Iye anapitiriza kuwauza kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano koma ine ndine wochokera kumwamba.+ Inu ndinu ochokera mʼdziko lino koma ine si wochokera mʼdziko lino. 24  Nʼchifukwa chake ndakuuzani kuti: Inu mudzafa mudakali ochimwa. Chifukwa ngati simukukhulupirira kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine, mudzafa mudakali ochimwa.” 25  Choncho iwo anayamba kunena kuti: “Kodi ndiwe ndani?” Yesu anayankha kuti: “Ndikudzivutitsiranji kulankhula ndi inu? 26  Ndili ndi zambiri zoti ndinene zokhudza inu nʼkupereka chiweruzo. Ndipotu amene anandituma ine amanena zoona, moti zimene ndinamva kwa iye ndi zimene ndikuzilankhula mʼdzikoli.”+ 27  Iwo sanazindikire kuti ankalankhula nawo zokhudza Atate. 28  Kenako Yesu anati: “Mukadzamukweza Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine+ komanso kuti sindichita chilichonse mongoganiza ndekha.+ Koma zimene ndimalankhula zimakhala zogwirizana ndendende ndi zimene Atate anandiphunzitsa. 29  Ndipo amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sanandisiye ndekha chifukwa ndimachita zinthu zimene zimamusangalatsa nthawi zonse.”+ 30  Pamene ankalankhula zimenezi, anthu ambiri anayamba kumukhulupirira. 31  Ndiyeno Yesu anapitiriza kuuza Ayuda amene anamukhulupirirawo kuti: “Mukapitiriza kusunga mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. 32  Mudzadziwa choonadi+ ndipo choonadi chidzakumasulani.”+ 33  Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu ndife ana a Abulahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu. Ndiye iwe ukunena bwanji kuti, ‘Mudzamasulidwaʼ?” 34  Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene akuchita tchimo ndi kapolo wa tchimo.+ 35  Komanso kapolo sakhala mʼnyumba ya mbuye wake kwamuyaya koma mwana ndi amene amakhalamo kwamuyaya. 36  Choncho ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka. 37  Ndikudziwa kuti ndinu mbadwa za Abulahamu. Koma mukufuna kundipha chifukwa simukuvomereza zimene ndikuphunzitsa. 38  Ine ndimalankhula zimene ndinaziona pamene ndinali ndi Atate wanga,+ koma inu mumachita zimene mwamva kwa atate wanu.” 39  Iwo anamuyankha kuti: “Atate wathu ndi Abulahamu.” Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala ana a Abulahamu,+ bwezi mukuchita ntchito za Abulahamu. 40  Koma tsopano mukufuna kundipha, munthu amene ndakuuzani choonadi chimene ndinachimva kwa Mulungu.+ Abulahamu sanachite zimenezi. 41  Inu mukuchita ntchito za atate wanu.” Iwo ananena kuti: “Ife sitinabadwe chifukwa cha chiwerewere,* tili ndi Atate mmodzi, Mulungu.” 42  Yesu anawauza kuti: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda,+ chifukwa ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwere mwakufuna kwanga koma Iyeyo ndi amene anandituma.+ 43  Nʼchifukwa chiyani simukumvetsa zimene ine ndikunena? Nʼchifukwa chakuti simukufuna kumvetsera mawu anga. 44  Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mukufuna kuchita zimene atate wanu amafuna.+ Iye ndi wopha anthu kuchokera pachiyambi+ ndipo sanapitirize kukhala mʼchoonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Akamanena bodza, amangosonyeza mmene alili, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.+ 45  Koma popeza ine ndimakuuzani zoona, simundikhulupirira. 46  Ndi ndani wa inu amene angapereke umboni wosonyeza kuti ndachita tchimo? Ngati ndimanena zoona, nʼchifukwa chiyani simundikhulupirira? 47  Wochokera kwa Mulungu amamvetsera mawu a Mulungu.+ Nʼchifukwa chake inu simumvetsera, chifukwa si inu ochokera kwa Mulungu.”+ 48  Ayudawo anamuyankha kuti: “Kodi tikunama tikamanena kuti, ‘Ndiwe Msamariya+ ndipo uli ndi chiwandaʼ?”+ 49  Yesu anayankha kuti: “Ine ndilibe chiwanda, koma ndikulemekeza Atate wanga ndipo inu mukundinyoza. 50  Komatu ine sindikudzifunira ndekha ulemerero.+ Mulungu ndi amene akufuna kuti ndilemekezedwe ndipo iye ndi woweruza. 51  Ndithudi ndikukuuzani, ngati munthu akusunga mawu anga, sadzaona imfa ngakhale pangʼono.”+ 52  Ayudawo ananena kuti: “Tsopano tadziwa kuti uli ndi chiwanda. Abulahamu anamwalira, chimodzimodzinso aneneri. Koma iwe ukunena kuti, ‘Ngati munthu akusunga mawu anga sadzalawa imfa ngakhale pangʼono.’ 53  Kodi iweyo ndiwe wamkulu kuposa atate wathu Abulahamu amene anamwalira? Aneneri nawonso anamwalira. Ndiye iweyo ukudziona ngati ndani?” 54  Yesu anayankha kuti: “Ngati ndikudzilemekeza ndekha, ndiye kuti ulemerero wanga ndi wopanda pake. Atate wanga ndi amene amandilemekeza,+ amene inu mukunena kuti ndi Mulungu wanu. 55  Chikhalirecho simukumudziwa,+ koma ine ndikumudziwa.+ Ngati ndinganene kuti sindikumudziwa ndingakhale wabodza ngati inu. Koma ndikumudziwa ndithu ndipo ndikusunga mawu ake. 56  Atate wanu Abulahamu ankasangalala kwambiri chifukwa ankayembekezera kuona tsiku langa, moti analionadi ndipo anasangalala.”+ 57  Kenako Ayudawo anati: “Sunakwanitse nʼkomwe zaka 50, ndiye ukuti unamuona Abulahamu?” 58  Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko, ine nʼkuti ndilipo kale.”+ 59  Choncho iwo anatola miyala kuti amugende nayo, koma Yesu anabisala nʼkutuluka mʼkachisimo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “potengera mfundo za anthu.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.