Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Otcheza Mchere ku Sahara

Anthu Otcheza Mchere ku Sahara

Anthu Otcheza Mchere ku Sahara

TINALI paulendo wa pagalimoto wopita kumudzi wina wotchedwa Teguidda-n-Tessoumt womwe uli pamtunda wamakilomita 200 kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa Agadez. M’mbali mwa msewu umene tinkadutsawo anazikamo mitengo yambiri. Kukakhala chimphepo chimene chimaulutsa mchenga, mitengo imeneyi imathandiza kuti munthu aziona msewu. Mphepo zoterezi zimachitikachitika kuno ku chipululu cha Sahara.

Msewu womwe timayendawu, kalekale munkadutsa ngamila zochokera ku mzinda wa Agadez womwe uli kumpoto kwa dziko la Niger, kupita ku Algeria. Kumudzi umene tinali kupitawu kuli mabanja 50 amene amatcheza mchere kuchokera m’dothi m’njira yochititsa chidwi kwambiri. Anthu a ku Sahara akhala akuchita zimenezi kwa zaka zambiri.

Mayiwe ndi Zulu Zopangidwa ndi Anthu

Titatsala pang’ono kufika ku mudziwu tinayamba kuona zulu kuchipululuku. Kenako munthu amene ankatiperekeza anaimitsa galimoto pafupi ndi chulu chachitali mamita 10 ndipo anatiuza kuti tikwere chulucho n’cholinga choti tione mudzi wonse. Tikukwera chuluchi munthuyu anatifotokozera kuti chulu chimenechi limodzi ndi zulu zinanso za kumaloku zinachita kupangidwa ndi anthu kuchokera ku dothi limene limatsala akamatcheza mchere.

Titafika pamwamba pa chuluchi, tinayamba kuona mudzi wonsewo ndipo tinaona kuti ndi malo okongola kwambiri. Pafupifupi chilichonse m’mudziwu, kungoyambira dothi, makoma a nyumba ndiponso madenga, zinkangooneka za katondo. Panali mitengo iwiri yokha imene inali yobiriwira ndipo inangoima ngati alonda a mudziwu. Wina unali koyambirira kwa mudziwu ndipo winawo unali ku mapeto kwake. Nyumba komanso mipanda ya kumeneku anaimanga ndi zidina. Nyumba zake zinali za mitundu yofanana koma pafupi ndi nyumbazi pali mayiwe otchezera mchere ambirimbiri ooneka mosiyanasiyana. Anthu a kumeneku nthawi zonse amakhala otanganidwa. Azibambo, azimayi ngakhalenso ana, onse amagwira ntchito mwakhama.

Kutcheza Mchere Mochititsa Chidwi

Tikutsika chuluchi, munthu amene ankatiperekeza uja anatifotokozera mmene anthuwo amatchezera mchere kuyambira kale. Iye anati: “Amakumba mayiwe amitundu iwiri, ena amakhala akuluakulu mwina pafupifupi mamita awiri ndipo ena amakhala ang’onoang’ono. M’mayiwe akuluakuluwa amathiramo madzi a mchere ndipo ang’onoang’ono amawagwiritsa ntchito poumitsira madziwo kuti patsale mchere wokhawokha. Kuderali kuli akasupe 20 ndipo madzi ake ndi amchere. Komatu chodabwitsa n’chakuti kwenikweni mcherewu umachokera m’dothi osati m’madziwa.” Kodi amatcheza bwanji mcherewu kuchokera m’dothili?

Tinaona bambo wina akuthira dothi pa dziwe lina lalikulu. Kenako anayamba kupondaponda padziwelo ngati akukanya matope oumbira zidina. Atamaliza anasiya madzi amatopewo kwa maola angapo kuti adikhe. Pafupi ndi dziweli panalinso mayiwe ena akuluakulu odzaza ndi madzi amatopewa. Madzi a m’dziwe lililonse ankaoneka mosiyanako pang’ono ndi madzi a m’mayiwe ena chifukwa choti m’maiwe onsewa matope amadikhanso mosiyanasiyana.

Pafupi ndi bamboyu panalinso bambo wina amene amayengula madzi amcherewa ndi chikho n’kumawathira m’mayiwe ang’onoang’ono. Amuna ndi amene amagwira ntchito imeneyi ndipo amaonetsetsanso kuti mayiwewa ali bwino. Mayiwe ena ndi achilengedwe, koma ena amachita kukumbidwa pathanthwe. M’madera ovuta kukumba, amaunjika dongo pathanthwe mozungulira kuti likhale khoma la dziwe. Kenako amadinda khomalo ndi ndodo kuti lilimbe. Mayiwe oterewa amafunika kuwakonza chaka ndi chaka.

Kodi nanga akazi amagwira ntchito yotani? Iwo amakanyamula dothi lamchere ndipo amaonetsetsa kuti nthawi zonse pali dothi lokwanira loti atchezere mchere. Komanso madzi akauma m’mayiwe ang’onoang’ono aja, iwo amachotsa mchere. Kenako amachotsa matope onse otsala kuti athiremonso madzi ndi dothi lina.

Nawonso ana amakhala yakaliyakali m’mayiwe ang’onoang’ono. Ntchito yawo ndi kuonetsetsa kuti madzi akuuma m’mayiwewo. Madziwo akamauma mchere umaundana pamwamba pamadziwo. Ndiye ukangosiyidwa umaphimba madzi a pansi pake ndipo sauma. Motero anawa amawaza madzi mchere woundanawu kuti usungunuke n’kupita pansi. Choncho madzi onse amauma n’kutsala mchere.

Koma n’chifukwa chiyani mayiwewa amaoneka amitundu yosiyanasiyana yokongola chonchi? Munthu amene amatiperekeza uja anafotokoza kuti: “M’dera limeneli muli dothi lamitundu itatu, ndiye madzi opezeka m’mayiwewo amatengera mtundu wa dothilo. Komanso mitunduyi imasiyana malingana ndi kuchuluka kwa mchere womwe uli m’madziwo. Kuwonjezera pamenepa, m’mayiwe ena mumamera ndere ndipo zimasintha maonekedwe a madzi.” Tinaonanso kuti dzuwa likamayenda, maonekedwe a madzi a m’mayiwewa amasinthanso.

Malonda a Mcherewu

Azimayi amatenga mcherewu usanaumitsitse n’kuumba timitanda timene amatiyanika padzuwa. Popeza mcherewu umakhala wosayenga timitandato timaonekabe toderako ngati dothi. Tinaona azimayi akuumba timitandati. Tina timakhala tooneka ngati mazira, tina ngati mpira ndipo tina timakhala tamakona atatu. Mayi wina anatiuza kuti amagulitsa timitanda tooneka ngati mazira ndiponso tooneka ngati mpira, koma amasunga tamakona atatu kuti adzapereke mphatso kwa anzawo.

Kodi ndani amagula mcherewu? Anthu oyendayenda komanso amalonda amene amadutsa m’mudziwu amagula mcherewu posinthanitsa ndi zakudya komanso zinthu zina. Mchere wambiri umakagulitsidwa ku misika ya m’mizinda ikuluikulu ya kumalire kwa chipululu. Kawirikawiri mchere wosayenga wa m’mudziwu suthiridwa m’zakudya za anthu koma m’zakudya za ziweto.

Tikubwerera komwe tinaimika galimoto yathu, tinaona bambo wina akuchotsa dothi pa dziwe lina. Ankanyamula dothilo n’kumaliunjika pa malo enaake ndipo umu ndi mmene zulu zakumeneku zimakulira. Pochoka kuderali tinkaganizirabe za mapiriwa. Tinaona kuti zuluzi zimapereka umboni wakuti kuyambira kalekale, mibadwo yosiyanasiyana ya anthu a ku Teguidda-n-Tessoumt yakhala ikugwira ntchito yotcheza mchere.—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa ndi munthu wina.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

“Chodabwitsa n’chakuti kwenikweni mcherewu umachokera m’dothi osati m’madziwa”

[Mapu patsamba 21]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

SAHARA

NIGER

Agadez

Teguidda-n-Tessoumt

[Mawu a Chithunzi]

Based on NASA/​Visible Earth imagery

[Chithunzi patsamba 23]

Kutcheza mchere m’dothi la ku Sahara

[Mawu a Chithunzi]

© Victor Englebert

[Chithunzi patsamba 23]

Mayiwe oumitsira mchere amaoneka amitundu yosiyanasiyana

[Mawu a Chithunzi]

© Ioseba Egibar/​age fotostock

[Chithunzi patsamba 23]

Kuumitsa timitanda ta mchere pa dzuwa